1 2Sam. 7.1-29 Ndipo pokhala Davide m'nyumba mwake, Davideyo anati kwa Natani mneneri, Taona, ndikhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la chipangano la Yehova likhala m'nsalu zotchinga.
2Ndipo Natani anati kwa Davide, Muchite zonse zili m'mtima mwanu; pakuti Mulungu ali nanu.
3Ndipo usiku womwewo mau a Mulungu anadzera Natani, ndi kuti,
4Kauze Davide mtumiki wanga, Atero Yehova, Usandimangire nyumba yokhalamo;
5pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinakwera naye Israele, kufikira lero lino; koma ndakhala ndikuyenda m'mahema uku ndi uku.
6Pali ponse ndinayenda nao Aisraele onse ndinanena kodi mau ndi woweruza aliyense wa Israele, amene ndinamuuza adyetse anthu anga, ndi kuti, Mwalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza?
7Chifukwa chake tsono, uzitero naye mtumiki wanga Davide, Atero Ambuye wa makamu, Ndinakutenga kubusa potsata iwe nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele;
8ndipo ndakhala ndi iwe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akulu okhala padziko.
9Ndipo ndaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka, kuti akhale m'malo mwao osasunthikanso; ndi ana osalungama sadzawapululanso monga poyamba paja;
10ndi kuyambira kuja ndinaika oweruza ayang'anire anthu anga Israele; ndipo ndagonjetsa adani ako onse. Ndikuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.
11Ndipo kudzachitika, atakwanira masiku ako kuti uzipita kukhala ndi makolo ako, ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, ndiye wa ana ako; ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.
12Iye adzandimangira nyumba; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wake kosatha.
13Ndidzakhala atate wake, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamchotsera chifundo changa monga muja ndinachotsera iye amene anakhala usanakhale iwe;
14Luk. 1.33koma ndidzamkhazikitsa m'nyumba mwanga, ndi m'ufumu wanga kosatha; ndi mpando wa chifumu wake udzakhazikika kosatha.
15Monga mwa mau awa onse, ndi monga mwa masomphenya awa onse, momwemo Natani analankhula ndi Davide.
Chonena Davide16Pamenepo mfumu Davide analowa nakhala pamaso pa Yehova, nati, Ndine yani, Yehova Mulungu, ndi nyumba yanga njotani kuti mwandifikitsa mpaka pano?
17Ndipo ichi nchaching'ono pamaso panu, Mulungu, koma mwanena za nyumba ya mtumiki wanu nthawi yam'tsogolo ndithu, ndipo mwandiyesera ngati munthu womveka, Yehova Mulungu.
18Anenenjinso Davide kwa inu za ulemu wochitikira mtumiki wanu? Pakuti mudziwa mtumiki wanu.
19Yehova, chifukwa cha mtumiki wanu, ndi monga mwa mtima wanu, mwachita ukulu uwu wonse, kundidziwitsa zazikulu izi zonse.
20Yehova, palibe wina wonga inu, palibenso Mulungu wina koma Inu; monga mwa zonse tazimva m'makutu mwathu.
21Ndiwo ayani akunga anthu anu Israele, mtundu wa pa wokha wa pa dziko lapansi, amene Mulungu anakadziombolera mtundu wa anthu, kudzibukitsira dzina, mwa zazikulu ndi zoopsa, pakupirikitsa amitundu pamaso pa anthu anu amene munawaombola m'Ejipito?
22Pakuti anthu anu Israele mudawayesa anthu anuanu kosatha; ndipo Inu, Yehova, munayamba kukhala Mulungu wao.
23Ndipo tsopano, Yehova, akhazikike kosalekeza mau mudanenawa za mtumiki wanu, ndi za nyumba yake, nimuchite monga mwanena.
24Inde likhazikike dzina lanu, likulitsidwe kosalekeza, ndi kuti, Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israele; akhalira Israele Mulungu; ndi nyumba ya Davide mtumiki wanu ikhazikika pamaso panu.
25Pakuti Inu, Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzammangira banja; momwemo mtumiki wanu waona mtima wakupemphera pamaso panu.
26Ndipo tsopano, Yehova, Inu ndinu Mulungu, ndipo mwanenera mtumiki wanu chokoma ichi;
27chakukomerani kudalitsa nyumba ya mtumiki wanu, kuti ikhalebe kosatha pamaso panu; pakuti Inu Yehova mwadalitsa, ndipo idzadalitsika kosatha.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.