1 2Maf. 20.3 Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda m'ungwiro wanga,
ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka.
2 Mas. 139.23 Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe;
yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.
3 2Maf. 20.3 Pakuti chifundo chanu chili pamaso panga;
ndipo ndayenda m'choona chanu.
4 Mas. 1.1; Yer. 15.17 Sindinakhala pansi ndi anthu achabe;
kapena kutsagana nao anthu othyasika.
5Ndidana nao msonkhano wa ochimwa,
ndipo sindidzakhala nao pansi ochita zoipa.
6 Deut. 21.6 Ndidzasamba manja anga mosalakwa;
kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova;
7kuti ndimveketse mau a chiyamiko,
ndi kulalikira ntchito zanu zonse zozizwa.
8 Mas. 27.4 Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu,
ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.
9Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa,
kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi;
10 Yes. 33.15-16 amene m'manja mwao muli mphulupulu,
ndi dzanja lao lamanja ladzala ndi zokometsera mlandu.
11Koma ine, ndidzayenda m'ungwiro wanga;
mundiombole, ndipo ndichitireni chifundo.
12 Mas. 40.2 Phazi langa liponda pachidikha,
m'masonkhano ndidzalemekeza Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.