1 Yes. 1.18; 3.13-14 Imvani mau a Yehova, inu ana a Israele; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe choonadi, kapena chifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko.
2Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.
3Amo. 5.16Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzachotsedwa.
4Koma munthu asatsutsane ndi mnzake, kapena kudzudzula mnzake; popeza anthu ako ndiwo akunga otsutsana ndi wansembe.
5Ndipo udzakhumudwa usana, ndi mneneri yemwe adzakhumudwa pamodzi ndi iwe usiku; ndipo ndidzaononga mai wako.
6Yes. 5.13Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.
71Sam. 2.30Monga anachuluka, momwemo anandichimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.
8Adyerera tchimo la anthu anga, nakhumbira chosalungama chao, yense ndi mtima wake.
9Yes. 24.2Ndipo kudzakhala monga anthu, momwemo wansembe; ndipo ndidzawalanga chifukwa chanjira zao, ndi kuwabwezera machitidwe ao.
10Ndipo adzadya, koma osakhuta; adzachita chigololo, koma osachuluka; pakuti waleka kusamalira Yehova.
11Yes. 28.7Chigololo, ndi vinyo, ndi vinyo watsopano, zichotsa mtima.
12Yes. 44.20; Hab. 2.19Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao.
13Yes. 57.5, 7; Aro. 1.28Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi minjali, ndi mkundi; popeza mthunzi wake ndi wabwino, chifukwa chake ana anu akazi achita uhule, ndi apongozi anu achita chigololo.
14Sindidzalanga ana anu akazi pochita iwo uhule, kapena apongozi anu pochita chigololo iwo; pakuti iwo okha apatukira padera ndi akazi achiwerewere, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa ku uhule; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa chamutu.
15Chinkana iwe, Israele, uchita uhule, koma asapalamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.
16Pakuti Israele wachita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwanawankhosa kuthengo lalikulu.
17Mat. 15.14Efuremu waphatikana ndi mafano, mlekeni.
18Chakumwa chao chasasa, achita uhule kosalekeza; akulu ao akonda manyazi kwambiri.
19Mphepo yamkulunga m'mapiko ake, ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.