2 MAFUMU 24 - Buku Lopatulika Bible 2014

1 2Mbi. 36.6 Masiku ake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwerako, Yehoyakimu nagwira mwendo wake zaka zitatu; pamenepo anatembenuka nampandukira.

2Yer. 25.9Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo.

32Maf. 21.2, 11, 16Zedi ichi chinadzera Yuda mwa lamulo la Yehova, kuwachotsa pamaso pake, chifukwa cha zolakwa za Manase, monga mwa zonse anazichita;

4ndiponso chifukwa cha mwazi wosachimwa adaukhetsa; popeza anadzaza Yerusalemu ndi mwazi wosachimwa; ndipo Yehova sanafune kukhululukira.

5Machitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

6Nagona Yehoyakimu ndi makolo ake, ndipo Yehoyakini mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.

7Yer. 37.5, 7Koma mfumu ya Aejipito sinabwerezanso kutuluka m'dziko lake, pakuti mfumu ya Babiloni idalanda kuyambira ku mtsinje wa Ejipito kufikira ku mtsinje Yufurate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aejipito.

Ayamba kutengedwa ukapolo kunka ku Babiloni

8Yehoyakini anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu; ndi dzina la make ndiye Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.

9Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adachita atate wake.

10Nthawi ija anyamata a Nebukadinezara mfumu ya Babiloni anakwerera Yerusalemu, naumangira mudziwo misasa.

11Nafika Nebukadinezara mfumu ya Babiloni kumudzi, ataumangira misasa anyamata ake,

12Yer. 29.1-2Ndipo Yehoyakini mfumu ya Yuda anatulukira kwa mfumu ya Babiloni, iye ndi make, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi adindo ake; mfumu ya Babiloni nimtenga chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.

132Maf. 20.17; Yes. 39.6Natulutsa kuchotsa komweko chuma chonse cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, naduladula zipangizo zonse zagolide adazipanga Solomoni mfumu ya Israele m'Kachisi wa Yehova, monga Yehova adanena.

14Yer. 24.1Nachoka nao a m'Yerusalemu onse, ndi akalonga onse, ndi ngwazi zonse, ndiwo andende zikwi khumi, ndi amisiri onse, ndi osula onse; sanatsale ndi mmodzi yense, koma anthu osauka okhaokha a m'dziko.

152Mbi. 36.10Nachoka naye Yehoyakini kunka naye ku Babiloni, ndi make wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ake, ndi omveka a m'dziko; anachoka nao andende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni.

16Ndi anthu amphamvu onse, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi amisiri, ndi osula chikwi chimodzi, onsewo achamuna oyenera nkhondo, omwewo mfumu ya Babiloni anadza nao andende ku Babiloni.

17Yer. 37.1Ndipo mfumu ya Babiloni analonga Mataniya mbale wa atate wake akhale mfumu m'malo mwake, nasanduliza dzina lake likhale Zedekiya.

Zedekiya mfumu yotsiriza ya Yuda

18 2Mbi. 36.11-13 Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.

19Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adachita Yehoyakimu.

20Ezk. 17.15Pakuti mwa mkwiyo wa Yehova zonse zidachitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda, mpaka adawataya pamaso pake; ndipo Zedekiya anapandukira mfumu ya Babiloni.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help