NUMERI 26 - Buku Lopatulika Bible 2014

Awerengedwa Aisraele

1Ndipo kunali, utatha mliriwo, Yehova ananena ndi Mose ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, nati,

2Werenga khamu lonse la ana a Israele, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, monga mwa nyumba za makolo ao, onse akutulukira kunkhondo m'Israele.

3Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Mowabu pa Yordani kufupi ku Yeriko, ndi kuti,

4Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israele, amene adatuluka m'dziko la Ejipito.

5 Gen. 46.8 Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israele; ana amuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;

6Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Karimi, ndiye kholo la banja la Akarimi.

7Iwo ndiwo mabanja a Arubeni; owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu.

8Mwana wamwamuna wa Palu ndiye Eliyabu.

9Num. 16.1Ndi ana a Eliyabu: Nemuwele, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, muja anatsutsana ndi Yehova;

101Ako. 10.6ndipo dziko linayasama pakamwa pake, ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, pakufa msonkhano uja; muja moto unaononga amuna mazana awiri ndi makumi asanu, nakhala iwo chizindikiro.

11Koma sanafe ana amuna a Kora.

12Ana amuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemuwele, ndiye kholo la banja la Anemuwele; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini;

13Zera, ndiye kholo la banja la Azera; Shaulo, ndiye kholo la banja la Ashaulo.

14Iwo ndiwo mabanja a Asimeoni, zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana ziwiri.

15Ana amuna a Gadi monga mwa mabanja ao ndiwo: Zefoni, ndiye kholo la banja la Azefoni; Hagi, ndiye kholo la banja la Ahagi; Suni, ndiye kholo la banja la Suni;

16Ozini, ndiye kholo la banja la Aozini; Eri, ndiye kholo la banja la Aeri;

17Arodi, ndiye kholo la banja la Aarodi; Areli, ndiye kholo la banja la Aareli.

18Iwo ndiwo mabanja a ana a Gadi, monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi anai ndi mazana asanu.

19Ana amuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m'dziko la Kanani.

20Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.

21Ndipo ana a Perezi ndiwo: Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Hamuli, ndiye kholo la banja la Ahamuli.

22Iwo ndiwo mabanja a Yuda monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu.

23Ana amuna a Isakara monga mwa mabanja ao ndiwo: Tola, ndiye kholo la banja la Atola; Puva, ndiye kholo la banja la Apuni;

24Yasubu, ndiye kholo la banja la Ayasubu; Simironi, ndiye kholo la banja la Asimironi.

25Iwo ndiwo mabanja a Isakara monga mwa owerengedwa ao; zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana atatu.

26Ana amuna a Zebuloni monga mwa mabanja ao ndiwo: Seredi, ndiye kholo la banja la Aseredi; Eloni, ndiye kholo la banja la Aeloni; Yaleele, ndiye kholo la banja la Ayaleele.

27Iwo ndiwo mabanja a Zebuloni monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu mazana asanu.

28Ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao ndiwo: Manase ndi Efuremu.

29Ana a Manase ndiwo: Makiri, ndiye kholo la banja la Amakiri; ndipo Makiri anabala Giliyadi; ndiye kholo la banja la Agiliyadi.

30Ana a Giliyadi ndiwo: Iyezere, ndiye kholo la banja la Aiyezere; Heleki, ndiye kholo la banja la Aheleki;

31ndi Asiriele, ndiye kholo la banja la Aasiriele; ndi Sekemu, ndiye kholo la banja la Asekemu;

32ndi Semida, ndiye kholo la banja la Asemida; ndi Hefere, ndiye kholo la banja la Ahefere.

33Num. 27.1Ndipo Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana akazi a Tselofekadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

34Iwo ndiwo mabanja ao a Manase; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.

35Ana amuna a Efuremu monga mwa mabanja ao ndiwo: Sutela, ndiye kholo la banja la Asutela; Bekere, ndiye kholo la banja la Abekere; Tahani, ndiye kholo la banja la Atahani.

36Ndipo mwana wamwamuna wa Sutela ndiye Erani, ndiye kholo la banja la Aerani.

37Iwo ndiwo mabanja a ana a Efuremu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao.

38Ana amuna a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiwo: Bela, ndiye kholo la banja la Abela; Asibele, ndiye kholo la banja la Aasibele; Ahiramu, ndiye kholo la banja la Aahiramu;

39Sefufamu ndiye kholo la banja la Asefufamu; Hufamu, ndiye kholo la banja la Ahufamu.

40Ndipo ana amuna a Bela ndiwo Aridi ndi Naamani; Aridi, ndiye kholo la banja la Aaridi; Naamani, ndiye kholo la banja la Anaamani.

41Iwo ndiwo ana a Benjamini monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi.

42Mwana wamwamuna wa Dani monga mwa mabanja ake ndiye Suhamu, ndiye kholo la banja la Asuhamu. Iwo ndiwo mabanja a Dani monga mwa mabanja ao.

43Mabanja onse a Asuhamu monga mwa owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana anai.

44Ana amuna a Asere monga mwa mabanja ao ndiwo: Imina, ndiye kholo la banja la Imina; Isivi, ndiye kholo la banja la Aisivi; Beriya, ndiye kholo la banja la Aberiya.

45Ana a Beriya ndiwo: Hebere, ndiye kholo la banja la Ahebere; Malikiele, ndiye kholo la banja la Amalikiele.

46Ndipo dzina la mwana wamkazi wa Asere ndiye Sera.

47Iwo ndiwo mabanja a ana amuna a Asere monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.

48Ana amuna a Nafutali monga mwa mabanja ao ndiwo: Yazeele, ndiye kholo la banja la Ayezeele; Guni, ndiye kholo la banja la Aguni;

49Yezere, ndiye kholo la banja la Ayezere; Silemu, ndiye kholo la banja la Asilemu.

50Iwo ndiwo mabanja a Nafutali, monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana anai.

51 Num. 1.46 Iwo ndiwo owerengedwa ao a ana a Israele, zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu.

Magawidwe a dziko

52Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

53Yos. 11.23Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale cholowa chao.

54Ochulukawo, uwachulukitsire cholowa chao; ochepawo uwachepetsere cholowa chao; ampatse yense cholowa chake monga mwa owerengedwa ake.

55Koma aligawe ndi kuchita maere; cholowa chao chikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao.

56Agawire ochuluka ndi ochepa cholowa chao monga mwa kuchita maere.

57Ndipo awa ndi owerengedwa ao a Alevi monga mwa mabanja ao: Geresoni, ndiye kholo la banja la Ageresoni; Kohati, ndiye kholo la banja la Akohati; Merari, ndiye kholo la banja la Amerari.

58Awa ndi mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, banja la Akora. Ndipo Kohati anabala Amuramu.

59Eks. 2.1-2Ndipo dzina lake la mkazi wake wa Amuramu ndiye Yokebede, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi m'Ejipito; ndipo iye anambalira Amuramu, Aroni ndi Mose, ndi Miriyamu mlongo wao.

60Lev. 10.1Ndipo Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara anabadwira Aroni.

61Koma Nadabu ndi Abihu adafa, muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova.

62Num. 1.49; 18.20Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwe pakati pa ana a Israele; chifukwa sanawapatse cholowa mwa ana a Israele.

63Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'zidikha za Mowabu ku Yordani pafupi pa Yeriko.

64Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'chipululu cha Sinai.

651Ako. 10.5-6Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help