YOBU 9 - Buku Lopatulika Bible 2014

Yobu avomereza ukulu wa Mulungu, koma okoma ndi oipa alangidwa mmodzimmodzi. Masautso ake amfunitsa kufa

1Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2 Aro. 3.20 Zoona, ndidziwa kuti chili chotero.

Koma munthu adzakhala wolungama bwanji kwa Mulungu?

3Akafuna Iye kutsutsana naye,

sadzambwezera Iye mau amodzi onse mwa chikwi.

4 Eks. 7.13 Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu;

ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?

5Ndiye amene asuntha mapiri, osachidziwa iwo,

amene amagubuduza mu mkwiyo wake.

6Amene agwedeza dziko lapansi lichoke m'malo mwake,

ndi mizati yake injenjemere.

7Amene alamulira dzuwa ndipo silituluka,

nakomera nyenyezi chizindikiro chakuzitsekera.

8Woyala thambo yekha,

naponda pa mafunde a panyanja.

9 Gen. 1.16 Wolenga Mlalang'amba, Akamwiniatsatana,

ndi Nsangwe, ndi Kumpotosimpita.

10Wochita zazikulu zosasanthulika,

ndi zodabwitsa zosawerengeka.

11Taona, Mulungu apita pali ine, koma sindimpenya;

napitirira, koma osamzindikira ine.

12Taona, akwatula, adzambwezetsa ndani?

Adzanena naye ndani, Mulikuchita chiyani?

13 Yes. 30.7 Mulungu sadzabweza mkwiyo wake;

athandizi odzikuza awerama pansi pa Iye.

14Nanga ine tsono ndidzamyankha bwanji,

ndi kusankha mau anga akutsutsana ndi Iye?

15Ameneyo, chinkana ndikadakhala wolungama,

sindikadamyankha;

ndikadangompembedza wondiweruza ine.

16Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye,

koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga.

17Pakuti andithyola ndi mkuntho,

nachulukitsa mabala anga kopanda chifukwa.

18Sandilola kuti ndipume,

koma andidzaza ndi zowawa.

19Tikanena za mphamvu, si ndiye wamphamvu?

Tikanena za kuweruza, adzamuitana ndani?

20Chinkana ndikhala wolungama,

pakamwa panga padzanditsutsa;

chinkana ndikhala wangwiro,

padzanditsutsa wamphulupulu.

21Chinkana ndikhala wangwiro, sindidzisamalira mwini,

ndipeputsa moyo wanga.

22 Ezk. 21.3 Kuli chimodzimodzi monsemo, m'mwemo ndikuti

Iye aononga wangwiro ndi woipa pamodzi.

23Mkwapulo ukapha modzidzimutsa,

adzaseka tsoka la wosachimwa.

24 2Sam. 15.30 Dziko lapansi laperekedwa m'dzanja la woipa;

aphimba maso a oweruza ake.

Ngati sindiye, pali yaninso?

25 Mas. 90.6-10 Tsopano masiku anga afulumira kuposa wamtokoma;

athawa osaona chokoma.

26Apitirira ngati zombo zaliwiro;

ngati mphungu igudukira chakudya chake.

27Ndikati, Ndidzaiwala chondidandaulitsa,

ndidzasintha nkhope yanga yachisoni, ndidzasekerera.

28Pamenepo ndiopa zisoni zanga zonse,

ndidziwa kuti simudzandiyesa wosachimwa.

29Mlandu udzanditsutsa;

potero ndigwire ntchito chabe chifukwa ninji?

30Ndikasamba madzi a chipale chofewa

ndi kuyeretsa manja anga ndi sopo.

31Mudzandiviikanso muli zoola,

ndi zovala zanga zidzanyansidwa nane.

32Pakuti sindiye munthu, monga ine, kuti ndimyankhe.

Kuti tikomane mlandu.

33Palibe wakutiweruza,

wakutisanjika ife tonse awiri manja ake.

34Andichotsere ndodo yake,

choopsa chake chisandichititse mantha;

35kuti ndinene, osamuopa,

pakuti sinditero monga umo ndili.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help