MASALIMO 58 - Buku Lopatulika Bible 2014

Davide adzudzula oipa Mulungu awalangeKwa Mkulu wa Nyimbo; pa Altasyeti; Mikitamu wa Davide.

1Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama?

Muweruza ana anthu molunjika kodi?

2Inde, mumtima muchita zosalungama;

pa dziko lapansi mugawira anthu chiwawa cha m'manja mwanu.

3 Mas. 51.5; Yes. 48.8 Oipa achita chilendo chibadwire,

asokera kuyambira kubadwa kwao, nanena bodza.

4 Mas. 140.3; Mlal. 10.11 Ululu wao ukunga wa njoka;

akunga mphiri yogontha m'khutu, itseka m'khutu mwake.

5Imene siimvera liu la oitana,

akuchita matsenga mochenjeratu.

6Thyolani mano ao m'kamwa mwao, Mulungu,

zulani zitsakano za misona ya mkango, Yehova.

7Apitetu ngati madzi oyenda;

popiringidza mivi yake ikhale yodukaduka.

8Apite ngati nkhono yosungunuka;

asaone dzuwa monga mtayo.

9Miphika yanu isanagwire moto waminga,

adzaiuluza, yaiwisi ndi yoyaka.

10 Mas. 52.6-7 Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango,

adzasamba mapazi ake m'mwazi wa woipa.

11 Mas. 98.9 Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama.

Indedi, pali Mulungu wakuweruza pa dziko lapansi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help