2 MAFUMU Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014

Mau OyambaBukuli likupitiriza kunena za mbiri ya mafumu a ku Israele ndi a ku Yuda. Bukuli lili ndi zigawo ziwiri: Gawo loyamba ndilo la maufumu awiri kuyambira pa chaka ngati cha 850 BC mpaka chaka cha 721 BC ndipo lachiwiri ndi la ufumu wa Yuda wokha, kufikira pa nthawi ya kupasuka kwa mzinda wa Yerusalemu chaka cha 586 BC.Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atazinga mzinda wa Yerusalemu nkuwuononga, anasankha Gedaliya kuti akhale bwanamkubwa woyang'anira dziko la Yuda m'dzina lake.Israele ndi Yuda, onse awiri adaonongeka chifukwa cha kusakhulupirika kwa mafumu ake ndi kwa anthu ao. Makamaka Ayuda ndiwo adakhumudwa kwambiri, poona kuti mzinda wa Yerusalemu wapasuka ndipo anthu ake ambiri atengedwa kupita ku ukapolo. Mneneri wotchuka pa masiku oyamba aja anali Elisa, amene adalowa m'malo mwa Eliya uja.Za mkatimuZa maufumu awiri aja 1.1—17.41

a. Mneneri Elisa 1.1—8.5

b. Mafumu a ku Yuda ndi mafumu a ku Israele 8.6—17.4

c. Kupasuka kwa mzinda wa Samariya 17.5-41

Za ufumu wa Yuda 18.1—24.20

a. Kuyambira Hezekiya mpaka Yosiya 18.1—21.26

b. Ufumu wa Yosiya 22.1—23.30

c. Mafumu otsiriza a Yuda 23.31—24.20

d. Kupasuka kwa mzinda wa Yerusalemu 25.1-30

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help