1Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa;
pondichepera mwandikulitsira malo.
Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
2Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti?
Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?
3 2Tim. 2.19 Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo,
adzamva Yehova m'mene ndimfuulira Iye.
4 2Ako. 13.5; Aef. 4.26 Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe.
Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.
5 Mas. 51.19 Iphani nsembe za chilungamo,
ndipo mumkhulupirire Yehova.
6 Num. 6.26 Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani?
Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
7 Yes. 9.3 Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga,
chakuposa chao m'nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao.
8 Mas. 3.5 Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo;
chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.