2 MBIRI 18 - Buku Lopatulika Bible 2014

Pangano pakati pa Yehosafati ndi Ahabu; afunsira kwa aneneri

1 2Mbi. 17.5 Yehosafati tsono anali nacho chuma ndi ulemu zomchulukira, nachita chibale ndi Ahabu.

21Maf. 22.2-25Ndipo zitatha zaka zina, anatsikira kwa Ahabu ku Samariya. Ndi Ahabu anamphera iye ndi anthu anali naye nkhosa, ndi ng'ombe zochuluka; namnyenga akwere naye pamodzi ku Ramoti Giliyadi.

3Nati Ahabu mfumu ya Israele kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, Mupita nane kodi ku Ramoti Giliyadi? Nayankha, nati, Monga inu momwemo ine; monga anthu anu momwemo anthu anga; tidzakhala nanu ku nkhondoyi.

4Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, Funsiranitu mau a Yehova lero lino.

5Pamenepo mfumu ya Israele anamemeza aneneri amuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Giliyadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m'dzanja la mfumu.

6Koma Yehosafati anati, Kulibenso kuno mneneri wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?

7Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Atsalanso munthu mmodzi, tifunsire Yehova kwa iye; koma ndimuda, pakuti sandinenera ine kanthu kokoma, koma zoipa nthawi zonse, ndiye Mikaya mwana wa Imila. Nati Yehosafati, Isatero mfumu.

8Pamenepo mfumu ya Israele inaitana mdindo, niti, Katenge msanga Mikaya mwana wa Imila.

9Mfumu ya Israele tsono ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zachifumu zao, nakhala pamalo popondera mphesa pakhomo pa chipata cha Samariya; ndi aneneri onse ananenera pamaso pao.

10Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi udzagunda Aaramu mpaka adatha psiti.

11Ndi aneneri onse ananenera momwemo, ndi kuti, Kwerani ku Ramoti Giliyadi, mudzapindulako; pakuti Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.

Mikaya anenera motsutsana nao

12Ndipo mthenga wakukaitana Mikaya ananena naye, ndi kuti, Taonani, mau a aneneri anenera mfumu chokoma ngati m'kamwa mmodzi; mau anu tsono akhaletu ngati amodzi a iwowa, nimunene chokoma.

13Num. 22.18, 20, 35Nati Mikaya, Pali Yehova, chonena Mulungu wanga ndidzanena chomwechi.

14Pamene anafika kwa mfumu, mfumu inanena naye, Mikaya timuke ku Ramoti Giliyadi kunkhondo kodi, kapena ndileke? Nati iye, Kwerani, mudzachita mwai; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lanu.

15Ndipo mfumu inati naye, Ndikulumbiritse kangati kuti unene nane choonadi chokhachokha m'dzina la Yehova?

16Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; nati Yehova, Awa alibe mbuye wao, abwerere yense kunyumba yake mumtendere.

17Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Sindinakuuzani kuti sadzandinenera zabwino koma zoipa?

18Nati iye, Chifukwa chake tamvani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lilikuima pa dzanja lake lamanja, ndi pa dzanja lake lamanzere.

19Nati Yehova, Adzamnyenga Ahabu mfumu ya Israele ndani, kuti akwereko, nagwe ku Ramoti Giliyadi? Nati wina mwakuti, wina mwakuti.

20Yob. 1.6Ndipo unatuluka mzimu, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Ndipo Yehova, ananena nao, Ndi chiyani?

21Nuti uwu, Ndidzatuluka ndi kukhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ake onse. Nati Iye, Udzamnyengadi, nudzakhoza; tuluka, ukatero kumene.

22Yes. 19.14; Ezk. 14.9Ndipo tsono taonani, Yehova analonga mzimu wabodza m'kamwa mwa aneneri anu awa, nakunenetserani choipa Yehova.

23Yer. 20.2; Mrk. 14.65; Mac. 23.2Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anayandikira, nampanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji kulankhula ndi iwe?

24Nati Mikaya, Tapenya, udzaona tsiku lolowa iwe m'chipinda cham'kati kubisala.

25Ndipo mfumu ya Israele inati, Mumtenge Mikaya, mukambweze kwa Amoni kazembe wa mudzi, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu;

262Mbi. 16.10nimuziti, Itero mfumu, Mumuike uyu m'kaidi, ndi kumdyetsa chakudya chomsautsa, ndi kumwetsa madzi omsautsa, mpaka ndikabwera mumtendere.

27Nati Mikaya, Mukakabwera ndi mtendere konse, Yehova sananene mwa ine. Nati iye, Tamverani, anthu inu nonsenu.

Nkhondo iwalaka naphedwa Ahabu

28Momwemo mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera kunka ku Ramoti Giliyadi.

29Ndi mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Ndidzadzizimbaitsa ndi kulowa kunkhondo, koma inu valani zovala zanu. Nidzizimbaitsa mfumu ya Israele, namuka iwo kunkhondo.

30Mfumu ya Aramu tsono idauza akapitao a magaleta ake, ndi kuti, Musayambana ndi ang'ono kapena akulu, koma ndi mfumu ya Israele yekha.

31Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israele. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anafuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapatukitsa amleke.

32Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona kuti sanali mfumu ya Israele anabwerera osamtsatanso.

33Ndipo munthu anaponya muvi wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israeleyo pakati pa maluma a malaya ake achitsulo. Potero anati kwa woyendetsa galetayo, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kukhamu la nkhondo kuno, pakuti ndalasidwa.

34Ndipo nkhondo inakula tsiku lija; koma mfumu ya Israele inagwirizizika m'galeta wake popenyana ndi Aaramu mpaka madzulo, namwalira nthawi yakulowa dzuwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help