YOBU 21 - Buku Lopatulika Bible 2014

Yobu ayankha kuti oipa ambiri amalemerera. Zooneka m'maso sizitiuza za mtima wa Mulungu

1Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2Mvetsetsani mau anga;

ndi ichi chikhale chitonthozo chanu.

3Mundilole, ndinene nanenso;

ndipo nditanena ine, sekani.

4Kodi ine, kudandaula kwanga, ndidandaulira munthu?

Ndipo ndilekerenji kupsa mtima?

5Ndiyang'anireni, nimusumwe,

gwirani pakamwa panu.

6Ndikangokumbukira ndivutika mtima,

ndi thupi langa lichita nyaunyau.

7 Yer. 12.1-2 Oipa akhaliranji ndi moyo,

nakalamba, nalemera kwakukulu?

8Mbeu zao zikhazikika pamodzi nao pankhope pao,

ndi ana ao pamaso pao.

9 Mas. 73.3, 5 Nyumba zao sizitekeseka ndi mantha,

ngakhale ndodo ya Mulungu siiwakhalira.

10Ng'ombe yao yamphongo imakwera, yosakanika;

ng'ombe yao yaikazi imaswa, yosapoloza.

11Atulutsa makanda ao ngati gulu,

ndi ana ao amavinavina.

12Aimbira lingaka ndi zeze,

nakondwera pomveka chitoliro.

13Atsekereza masiku ao ndi zokoma,

natsikira m'kamphindi kumanda.

14Koma adati kwa Mulungu, Tichokereni;

pakuti sitifuna kudziwa njira zanu.

15 Eks. 5.2 Wamphamvuyonse ndiye yani kuti timtumikire?

Ndipo tidzapindulanji pakumpemphera Iye?

16 Mas. 1.1 Taonani, zokoma zao sizili m'dzanja lao;

(koma uphungu wa oipa unditalikira.)

17Ngati nyali za oipa zizimidwa kawirikawiri?

Ngati tsoka lao liwagwera?

Ngati Mulungu awagawira zowawa mu mkwiyo wake?

18 Mas. 1.4 Ngati akunga ziputu zomka ndi mphepo,

ngati mungu wouluzika ndi nkuntho?

19Mukuti, Mulungu asungira ana ake a munthu choipa chake,

ambwezere munthuyo kuti achidziwe.

20 Yes. 51.17; Yer. 25.15; Chiv. 14.10 Aone yekha chionongeko chake m'maso mwake,

namwe mkwiyo wa Wamphamvuyonse.

21Pakuti chomsamalitsa nyumba yake nchiyani, atapita iye,

chiwerengo cha miyezi yake chitadulidwa pakati?

22 Yes. 40.13-14; Aro. 11.34 Ngati pali munthu wakumphunzitsa Mulungu nzeru?

Popeza Iye aweruza mlandu iwo okwezeka.

23Wina akufa, wabiriwiri,

ali chikhalire ndi chipumulire.

24Mbale zake zidzala ndi mkaka;

ndi wongo wa m'mafupa ake uli momwe.

25Koma mnzake akufa ali nao mtima wakuwawa,

osalawa chokoma konse.

26Iwo agona chimodzimodzi kufumbi,

ndi mphutsi ziwakuta.

27Taonani, ndidziwa maganizo anu,

ndi chiwembu mundilingirira moipa.

28Pakuti munena, Ili kuti nyumba ya kalonga?

Ndi hema wokhalamo woipa ali kuti?

29Simunawafunsa kodi opita m'njira?

Ndipo simusamalira zotsimikiza zao?

30 Miy. 16.4; 2Pet. 2.9 Zakuti munthu woipa asungika tsiku la tsoka?

Natulutsidwa tsiku la mkwiyo?

31Adzamfotokozera ndani njira yake pamaso pake?

Nadzamlipitsa ndani pa ichi anachichita?

32Potsiriza pake adzapita naye kumanda,

nadzadikira pamanda pake.

33 Aheb. 9.27 Zibuma za kuchigwa zidzamkomera.

Adzakoka anthu onse amtsate,

monga anamtsogolera osawerengeka.

34Potero munditonthozeranji nazo zopanda pake,

popeza m'mayankho mwanu mutsala mabodza okha?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help