AKOLOSE 2 - Buku Lopatulika Bible 2014

1 Akol. 1.29 Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndili nayo chifukwa cha inu, ndi iwowa a m'Laodikea, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m'thupi;

2Akol. 3.14kuti itonthozeke mitima yao, nalumikizike pamodzi iwo m'chikondi, kufikira chuma chonse cha chidzalo cha chidziwitso, kuti akazindikire iwo chinsinsi cha Mulungu, ndiye Khristu,

31Ako. 1.24amene zolemera zonse za nzeru ndi chidziwitso zibisika mwa Iye.

Asatsate ziphunzitso zonyenga

4Ichi ndinena, kuti munthu asakusokeretseni inu ndi mau okopakopa.

51Pet. 5.9Pakuti ndingakhale ndili kwina m'thupi, komatu mumzimu ndili pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi chilimbiko cha chikhulupiriro chanu cha kwa Khristu.

6 1Ate. 4.1 Chifukwa chake monga momwe munalandira Khristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye,

7Aef. 2.21-22ozika mizu ndi omangirika mwa Iye, ndi okhazikika m'chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa chiyamiko.

8 Yer. 29.8 Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;

9Yoh. 1.14pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m'thupi,

10Yoh. 1.16ndipo muli odzazidwa mwa Iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro;

11Aro. 6.6; Afi. 3.3amenenso munadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m'mavulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Khristu;

12Aro. 6.4-5popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi Iye m'chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa Iye kwa akufa.

13Aef. 2.1, 5-7Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse;

14Aef. 2.15-16adatha kutifafanizira cha pa ifecho cholembedwa m'zoikikazo, chimene chinali chotsutsana nafe: ndipo anachichotsera pakatipo, ndi kuchikhomera ichi pamtanda;

15Gen. 3.15; Yoh. 12.31; 16.11atavula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako.

16Chifukwa chake munthu aliyense asakuweruzeni inu m'chakudya, kapena chakumwa, kapena m'kunena tsiku la chikondwerero, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata;

17Aheb. 8.5; 9.9ndizo mthunzi wa zilinkudzazo; koma thupi ndi la Khristu.

18Akol. 2.4Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake, wosagwiritsa mutuwo,

19Aef. 4.15-16kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.

20 Agal. 2.19 Ngati munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nazo zoyamba za dziko lapansi, mugonjeranji kuzoikikazo, monga ngati moyo wanu mukhala nao m'dziko lapansi,

211Tim. 4.3usaikapo dzanja, usalawa, usakhudza,

22(ndizo zonse zakuonongedwa pochita nazo), monga mwa malangizo ndi maphunziro a anthu?

231Tim. 4.8Zimene zili naotu manenedwe a nzeru m'kutumikira kwa chifuniro cha mwini wake, ndi kudzichepetsa, ndi kusalabadira thupi; koma zilibe mphamvu konse yakuletsa chikhutitso cha thupi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help