NUMERI 2 - Buku Lopatulika Bible 2014

Malongosoledwe a chigono

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2Ana a Israele azimanga mahema ao yense ku mbendera yake, ya chizindikiro cha nyumba ya kholo lake; amange mahema ao popenyana ndi chihema chokomanako pozungulira.

3Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.

4Ndipo khamu lake, ndi owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri, mphambu zinai, kudza mazana asanu ndi limodzi.

5Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Isakara; ndipo kalonga wa ana a Isakara ndiye Netanele mwana wa Zuwara.

6Ndipo khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai.

7Ndi fuko la Zebuloni: kalonga wa ana a Zebuloni ndiye Eliyabu mwana wa Heloni.

8Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai.

9Owerengedwa onse a chigono cha Yuda ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi mphambu mazana anai, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsogolera ulendo.

10Mbendera ya chigono cha Rubeni ikhale kumwera monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Rubeni ndiye Elizuri mwana wa Sedeuri.

11Ndi khamu lake, ndi olembedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu.

12Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Simeoni; ndi kalonga wa ana a Simeoni ndiye Selumiele mwana wa Zurishadai.

13Ndi khamu lake ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu.

14Ndi fuko la Gadi; kalonga wa ana a Gadi ndiye Eliyasafu mwana wa Reuwele.

15Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu.

16Owerengedwa onse a chigono cha Rubeni ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi chimodzi kudza mazana anai mphambu makumi asanu, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsatana nao otsogolerawo.

17Pamenepo khamu la Alevi azimuka nacho chihema chokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pake, monga mwa mbendera zao.

18Mbendera ya chigono cha Efuremu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efuremu ndiye Elisama mwana wa Amihudi.

19Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai kudza mazana asanu.

20Ndipo oyandikizana naye ndiwo a fuko la Manase; ndi kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliele mwana wa Pedazuri.

21Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri.

22Ndi fuko la Benjamini: kalonga wa ana a Benjamini ndiye Abidani mwana wa Gideoni.

23Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai.

24Owerengedwa onse a chigono cha Efuremu ndiwo zikwi makumi khumi mphambu zisanu ndi zitatu kudza zana limodzi, monga mwa makamu ao. Iwo ndiwo aziyenda gulu lachitatu paulendo.

25Mbendera ya chigono cha Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai.

26Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.

27Ndipo iwo a kumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Asere; ndi kalonga wa ana a Asere ndiye Pagiyele mwana wa Okarani.

28Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu chimodzi kudza mazana asanu.

29Ndi fuko la Nafutali: ndi kalonga wa ana a Nafutali ndiye Ahira mwana wa Enani.

30Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.

31Owerengedwa onse a chigono cha Dani ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi. Iwo ndiwo aziyenda m'mbuyo paulendo, monga mwa mbendera zao.

32Amenewo ndiwo anawerengedwa a ana a Israele monga mwa nyumba za makolo ao; owerengedwa onse a m'zigono, monga mwa makamu ao, ndiwo zikwi makumi khumi kasanu ndi kamodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.

33Koma sanawerenge Alevi mwa ana a Israele; monga Yehova adauza Mose.

34Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help