1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2Nena ndi Aroni, ndi ana ake amuna, ndi ana a Israele onse, nuti nao, Ichi ndi chimene Yehova wauza, ndi kuti,
3Munthu aliyense wa mbumba ya Israele akapha ng'ombe, kapena mwanawankhosa, kapena mbuzi, m'chigono, kapena akaipha kunja kwa chigono,
4osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti aipereke chopereka cha Yehova, ku bwalo la Kachisi wa Yehova; azimuyesa munthuyu wochimwira mwazi, wakhetsa mwazi; ndipo amsadze munthuyo kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake;
5kotero kuti ana a Israele azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova.
6Ndipo wansembeyo awaze mwaziwo pa guwa la nsembe la Yehova, pa khomo la chihema chokomanako, natenthe mafuta akhale fungo lokoma lokwera kwa Yehova.
7Ndipo asamapheranso milungu ina nsembe zao, zimene azitsata ndi chigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.
8Ndipo uzinena nao, Munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wakugonera pakati panu, amene apereka nsembe yopsereza kapena nsembe yophera,
9osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.
Aletsedwa kudya mwazi10 Gen. 9.4 Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.
11Mat. 26.28; Aheb. 9.22Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake.
12Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israele, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu, kapena mlendo aliyense wakugonera mwa inu asamadya mwazi.
13Ndipo munthu aliyense wa ana a Israele, kapena mlendo wakugonera pakati pa inu, akasaka nyama kapena mbalame yakudya, nakaigwira; azikhetsa mwazi wake, naufotsere ndi dothi.
14Gen. 9.4Pakuti ndiwo moyo wa nyama zonse, mwazi wake ndiwo moyo wake; chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israele, Musamadya mwazi wa nyama iliyonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wake; aliyense akaudya adzasadzidwa.
15Ezk. 44.31Ndipo aliyense wakudya yakufa yokha, kapena yojiwa kuthengo, ngakhale ndiye wa m'dziko kapena mlendo, azitsuka nsalu zake, nasambe ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo adzakhala woyera.
16Koma akapanda kuzitsuka, kapena kusamba thupi lake, adzasenza mphulupulu yake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.