MALIRO 3 - Buku Lopatulika Bible 2014

Yeremiya achita nkhawa, adziponya kwa Yehova

1Ine ndine munthuyu wakuona msauko ndi ndodo ya ukali wake.

2Wanditsogolera, nandiyendetsa mumdima, si m'kuunika ai.

3Zoonadi amandibwezerabwezera dzanja lake

monditsutsa tsiku lonse.

4Wagugitsa thupi langa ndi khungu langa,

nathyola mafupa anga.

5Wandimangira zithando za nkhondo,

wandizinga ndi ulembe ndi mavuto.

6Wandikhalitsa mumdima ngati akufa kale.

7Wanditsekereza ndi guta, sindingatuluke;

walemeretsa unyolo wanga.

8

ngati zinyalala ndi za kudzala.

46Adani athu onse anatiyasamira.

47Mantha ndi dzenje zitifikira, ndi phokoso ndi chionongeko.

48 Mali. 2.11 M'diso mwanga mutsika mitsinje ya madzi

chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga woonongedwa.

49Diso langa lingotsanulira osaleka, osapumula,

50kufikira Yehova adzazolika kumwamba ndi kuona.

51Diso langa limvetsa moyo wanga zowawa

chifukwa cha ana akazi onse a m'mudzi mwanga.

52 Mas. 35.7 Ondida opanda chifukwa anandiinga ngati mbalame;

53 Yer. 38.6, 9-10 anaononga moyo wanga m'dzenje,

naponya mwala pamwamba pa ine;

54madzi anayenda pamwamba pa mutu panga,

ndinati, Ndalikhidwa.

55 Yon. 2.2 Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndili m'dzenje lapansi;

56munamva mau anga;

musabise khutu lanu popuma ndi pofuula ine.

57 Yak. 4.8 Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati, Usaope.

58 1Sam. 24.15 Ambuye munanenera moyo wanga milandu yake; munaombola moyo wanga.

59Yehova, mwaona choipa anandichitiracho, mundiweruzire.

60Mwaona kubwezera kwao konse

ndi zopangira zao zonse za pa ine.

61Mwamva chitonzo chao, Yehova,

ndi zopangira zao zonse za pa ine,

62milomo ya akutsutsana nane

ndi zolingalira zao za pa ine tsiku lonse.

63Taonani kukhala ndi kunyamuka kwao; ndine nyimbo yao.

64 2Tim. 4.14 Mudzawabwezera chilango, Yehova,

monga mwa machitidwe a manja ao.

65Muphimbe mtima wao ndi kuwatemberera;

66mudzawalondola mokwiya

ndi kuwaononga pansi pa thambo la Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help