NAHUMU 3 - Buku Lopatulika Bible 2014

Zoipa za Ninive ndi kupasuka kwake

1 Hab. 2.12 Tsoka mudzi wa mwazi! Udzala nao mabodza ndi zachifwamba; zachifwamba sizidukiza.

2Kumveka kwa chikoti, ndi mkokomo wa kuyenda kwa njinga za magaleta; ndi kaphatakaphata wa akavalo, ndi gwegwegwe wa magaleta;

3munthu wokwera pa kavalo, ndi lupanga lonyezimira, ndi mkondo wong'anipa; ndi aunyinji ophedwa, ndi chimulu cha mitembo, palibe kutha zitanda; angokhumudwa ndi zitanda;

4chifukwa cha chiwerewere chochuluka cha wachiwerewere wokongola, ndiye mkaziyo mwini nyanga, wakugulitsa amitundu mwa chiwerewere chake, ndi mabanja mwa nyanga zake.

5Nah. 2.13Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndidzaphimba nkhope yako ndi nsalu yako yoyesa mthendene; ndipo ndidzaonetsa amitundu umaliseche wako, ndi mafumu manyazi ako.

6Mala. 2.9Ndipo ndidzakuponyera zonyansa, ndi kukuchititsa manyazi, ndi kukuika chopenyapo.

7Chiv. 18.10Ndipo kudzali kuti onse akupenyerera iwe adzakuthawa, nadzati, Ninive wapasuka, adzamlira maliro ndani? Ndidzakufunira kuti akukutonthoza?

8Yer. 46.25Kodi uli wabwino woposa No-Amoni, wokhala pakati pa mitsinje wozingidwa ndi madzi; amene tchemba lake ndilo nyanja, ndi linga lake ndilo nyanja?

9Kusi ndi Ejipito ndiwo mphamvu yake, ndiyo yosatha, Puti ndi Libiya ndiwo akukuthandiza.

10Yes. 13.16Koma iye anatengedwa, analowa ndende; ana ake a makanda anaphwanyika polekeza pake pa miseu yake yonse; ndi pa omveka ake anachita maere, ndi akulu ake onse anamangidwa maunyolo.

11Iwenso udzaledzera, udzabisala; iwenso udzafunanso polimbikira chifukwa cha mdani.

12Chiv. 6.13Malinga ako onse adzanga mikuyu ndi nkhuyu zoyamba kupsa; akagwedeza zingokugwa m'kamwa mwa wakudya.

13Yer. 50.37Taona, anthu ako m'kati mwako akunga akazi, zipata za dziko lako zatsegulidwira adani ako papakulu; moto watha mipingiridzo yako.

14Udzitungiretu madzi a nthawi yokumangira misasa, limbikitsa malinga ako, lowa kuthope, ponda dothi, limbitsa ng'anjo yanjerwa.

15Yow. 1.4, 6Pomwepo moto udzatha iwe; lupanga lidzakuononga; lidzatha iwe ngati chirimamine; udzichulukitse ngati chirimamine, udzichulukitse ngati dzombe.

16Wachulukitsa amalonda ako koposa nyenyezi za kuthambo; chirimamine anyambita, nauluka, nathawa.

17Chiv. 9.7Ovala korona ako akunga dzombe, ndi akazembe, ndi akazemba ako ngati ziwalamsatsi zakutera m'matchinga tsiku lachisanu, koma likafundukula dzuwa ziuluka nizithawa, ndi kumene zinakhalako sikudziwikanso.

18Mas. 76.6Abusa ako aodzera, mfumu ya ku Asiriya; omveka ako apumula; anthu ako amwazika pamapiri, ndipo palibe wakuwasonkhanitsa.

19Mik. 1.9; Zef. 2.15Palibe chakulunzitsa kuthyoka kwako; bala lako liwawa; onse akumva mbiri yako akuombera manja; pakuti ndaniyo kuipa kwako sikunampitapitabe?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help