CHIVUMBULUTSO 3 - Buku Lopatulika Bible 2014

Kalata wachisanu wa kwa Mpingo wa ku Sardi

1 1Tim. 6.20; Chiv. 1.4 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba:

Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.

2Khala wodikira, ndipo limbitsa zotsalira zimene zinafuna kufa; pakuti sindinapeza ntchito zako zakufikira pamaso pa Mulungu wanga.

3Mat. 24.42-43; 1Tim. 6.20Chifukwa chake kumbukira umo unalandira nunamvamo; nusunge nulape. Ukapanda kudikira tsono, ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yake ndidzadza pa iwe.

4Chiv. 6.11Komatu uli nao maina owerengeka m'Sardi, amene sanadetsa zovala zao; ndipo adzayenda ndi Ine m'zoyera; chifukwa ali oyenera.

5Eks. 32.32; Chiv. 19.8Iye amene alakika adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m'buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.

6Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Kalata wachisanu ndi chimodzi, wa kwa Mpingo wa ku Filadelfiya

7 Yes. 22.22; Mac. 3.14 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfiya lemba:

Izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:

81Ako. 16.9Ndidziwa ntchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sakhoza kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.

9Yes. 49.23; Chiv. 2.9Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.

102Pet. 2.9Popeza unasunga mau a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza pa dziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.

11Chiv. 3.3Ndidza msanga; gwira chimene uli nacho, kuti wina angalande korona wako.

12Agal. 2.9; Chiv. 2.17Iye wakupambana, ndidzamyesa iye mzati wa m'Kachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika m'Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.

13Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Kalata wachisanu ndi chiwiri, wa kwa Mpingo wa ku Laodikea

14 Chiv. 1.5 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikea lemba:

Izi anena Ameni'yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu:

15Ndidziwa ntchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha.

16Kotero, popeza uli wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulavula m'kamwa mwanga.

17Hos. 12.8-11Chifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndili nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa;

18Yes. 55.1; Mat. 13.44; Chiv. 16.15; 19.8ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.

19Aheb. 12.5-6Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.

20Luk. 12.36-37; Yoh. 14.23Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.

21Luk. 22.30Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinalakika, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.

22Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help