MASALIMO 107 - Buku Lopatulika Bible 2014

Olanditsidwa, alendo, omangidwa, odwala, amalinyero ndi onse ena alemekeze Yehova

1 Mas. 106.1 Yamikani Yehova pakuti Iye ndiye wabwino;

pakuti chifundo chake nchosatha.

2Atere oomboledwa a Yehova,

amene anawaombola m'dzanja la wosautsa;

3 Yes. 43.5-6 nawasokolotsa kumaiko,

kuchokera kum'mawa ndi kumadzulo,

kumpoto ndi kunyanja.

4 Deut. 32.10 Anasokera m'chipululu, m'njira yopanda anthu;

osapeza mudzi wokhalamo.

5Anamva njala ndi ludzu,

moyo wao unakomoka m'kati mwao.

6 Mas. 50.15 Mas. 60.5-12 Pamenepo anafuulira kwa Yehova mumsauko mwao,

ndipo anawalanditsa m'kupsinjika kwao.

7 Ezr. 8.21 Ndipo anawatsogolera pa njira yolunjika,

kuti amuke kumudzi wokhalamo.

8Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake,

ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!

9 Mas. 34.10; Luk. 1.53 Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka,

nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.

10 Luk. 1.79 Iwo akukhala mumdima ndi mu mthunzi wa imfa,

omangika ndi kuzunzika ndi chitsulo;

11popeza anapikisana nao mau a Mulungu,

napeputsa uphungu wa Wam'mwambamwamba;

12kotero kuti anagonjetsa mtima wao ndi chovuta;

iwowa anakhumudwa koma panalibe mthandizi.

13 Mas. 107.6, 19, 28 Pamenepo anafuulira kwa Yehova mumsauko mwao,

ndipo anawapulumutsa m'kupsinjika kwao.

14 Mac. 12.7-11 Anawatulutsa mumdima ndi mu mthunzi wa imfa,

nadula zomangira zao.

15 Mas. 107.8, 21, 31 Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake,

ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!

16 Yes. 45.2 Popeza adaswa zitseko zamkuwa,

nathyola mipiringidzo yachitsulo.

17 Mali. 3.39 Anthu opusa azunzika chifukwa cha zolakwa zao,

ndi chifukwa cha mphulupulu zao.

18Mtima wao unyansidwa nacho chakudya chilichonse;

ndipo ayandikira zipata za imfa.

19Pamenepo afuulira kwa Yehova m'kusauka kwao,

ndipo awapulumutsa m'kupsinjika kwao.

20 2Maf. 20.4-5 Atumiza mau ake nawachiritsa,

nawapulumutsa ku chionongeko chao.

21Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake,

ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!

22 Mas. 50.14-15 Ndipo apereke nsembe zachiyamiko,

nafotokozere ntchito zake ndi kufuula mokondwera.

23Iwo akutsikira kunyanja nalowa m'zombo,

akuchita ntchito zao pa madzi aakulu.

24Iwowa apenya ntchito za Yehova,

ndi zodabwitsa zake m'madzi ozama.

25 Yon. 1.4 Popeza anena, nautsa namondwe,

amene autsa mafunde ake.

26Akwera kuthambo, atsikira kozama;

mtima wao usungunuka nacho choipacho.

27Adzandira napambanitsa miyendo ngati munthu woledzera,

nathedwa nzeru konse.

28Pamenepo afuulira kwa Yehova m'kusauka kwao,

ndipo awatulutsa m'kupsinjika kwao.

29 Mat. 8.26 Asanduliza namondwe akhale bata,

kotero kuti mafunde ake atonthole.

30Pamenepo akondwera, popeza pagwa bata;

ndipo Iye awatsogolera kudooko afunako.

31Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake,

ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!

32 Mas. 22.22, 25 Amkwezenso mu msonkhano wa anthu,

namlemekeze pokhala akulu.

33 1Maf. 17.1, 7 Asanduliza mitsinje ikhale chipululu,

ndi akasupe a madzi akhale nthaka youma.

34 Gen. 19.24-28 Dziko la zipatso, likhale lakhulo,

chifukwa cha choipa cha iwo okhalamo.

35 Yes. 41.18 Asanduliza chipululu chikhale thawale,

ndi dziko louma likhale akasupe a madzi.

36Ndi apo akhalitsa anjala,

kuti amangeko mudzi wokhalamo anthu;

37nafese m'minda, naoke mipesa,

ndiyo yakubala zipatso zolemeza.

38 Eks. 1.7 Ndipo awadalitsa, kotero kuti achuluka kwambiri;

osachepsanso zoweta zao.

39 2Maf. 10.32 Koma achepanso, nawerama,

chifukwa cha chisautso, choipa ndi chisoni.

40Atsanulira chimpepulo pa akulu,

nawasokeretsa m'chipululu mopanda njira.

41 1Sam. 2.8 Koma aika waumphawi pamsanje posazunzika,

nampatsa mabanja ngati gulu la nkhosa.

42 Aro. 3.19 Oongoka mtima adzachiona nadzasekera;

koma chosalungama chonse chitseka pakamwa pake.

43 Hos. 14.9 Wokhala nazo nzeru asamalire izi,

ndipo azindikire zachifundo za Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help