1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse Kachisi wa chihema chokomanako.
3Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nuchinge likasalo ndi nsalu yotchingayo.
4Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikapo nyalicho, ndi kuyatsa nyali zake.
5Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lagolide chakuno cha likasa la mboni, numange pa Kachisi nsalu yotsekera pakhomo.
6Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako.
7Ukaikenso mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.
8Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo.
9Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nao Kachisi, ndi zonse zili m'mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse; ndipo adzakhala wopatulika.
10Eks. 29.37Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zake zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulika kwambiri.
11Udzozenso mkhate ndi tsinde lake, ndi kuupatula.
12Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake amuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa ndi madzi.
13Nuveke Aroni chovala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatula andichitire Ine ntchito ya nsembe.
14Ndipo ubwere nao ana ake amuna ndi kuwaveka malaya am'kati;
15nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andichitire ntchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao.
16Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.
17 Num. 7.1 Ndipo kunali, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa Kachisi,
18ndipo Mose anautsa Kachisi, nakhazika makamwa ake, naimika matabwa ake, namangapo mitanda yake, nautsa mizati ndi nsanamira zake.
19Ndipo anayalika hema pamwamba pa Kachisi, naika chophimba cha chihema pamwamba pake; monga Yehova adamuuza Mose.
20Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa;
21nalowa nalo likasa m'Kachisi, napachika nsalu yotchinga, natchinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose.
22Ndipo anaika gomelo m'chihema chokomanako, pa mbali ya kumpoto ya Kachisi, kunja kwa nsalu yotchinga.
23Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
24Ndipo anaika choikapo nyali m'chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi.
25Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
26Ndipo anaika guwa la nsembe lagolide m'chihema chokomanako chakuno cha nsalu yotchinga;
27nafukizapo chofukiza cha fungo lokoma; monga Yehova adamuuza Mose.
28Ndipo anapachika ku Kachisi nsalu yotsekera pakhomo.
29Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose.
30Ndipo anaika mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba.
31Ndipo Mose ndi Aroni ndi ana ake amuna anasamba manja ao ndi mapazi ao m'menemo;
32pakulowa iwo m'chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.
33Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa chihema ndi guwa la nsembe, napachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza ntchitoyi.
34 Num. 9.15; 1Maf. 8.10; Chiv. 15.8 Pamenepo mtambo unaphimba chihema chokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisiyo.
35Ndipo Mose sanathe kulowa m'chihema chokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.
36Num. 9.19-22Ndipo pakukwera mtambo kuchokera ku Kachisi, ana a Israele amayenda maulendo ao onse;
37koma ukapanda kukwera mtambo, samayenda ulendo wao kufikira tsiku loti wakwera.
38Num. 14.14; Neh. 9.19; Mas. 78.14; 1Ako. 10.1Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pa Kachisi msana, ndi usiku munali moto m'menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israele, m'maulendo ao onse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.