MASALIMO 56 - Buku Lopatulika Bible 2014

Davide apempha Mulungu amlanditse; ayamika atamlanditsaKwa Mkulu wa Nyimbo; pa Yonat-Elem-Rekokimu. Mikitamu wa Davide, muja Afilisti anamgwira m'Gati.

1 Mas. 57.1 Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza.

Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.

2 Mas. 57.3 Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse,

pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza.

3Tsiku lakuopa ine,

ndidzakhulupirira Inu.

4 Yes. 51.12; Aheb. 13.6 Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake,

ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa;

anthu adzandichitanji?

5Tsiku lonse atenderuza mau anga,

zolingirira zao zonse zili pa ine kundichitira choipa.

6 Mas. 59.3 Amemezana, alalira,

atchereza mapazi anga,

popeza alindira moyo wanga.

7Kodi adzapulumuka ndi zopanda pake?

Gwetsani anthu mumkwiyo, Mulungu.

8 2Maf. 20.5; Mlal. 3.16 Muwerenga kuthawathawa kwanga,

sungani misozi yanga m'nsupa yanu;

kodi siikhala m'buku mwanu?

9 Aro. 8.31 Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine.

Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.

10Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake,

mwa Yehova ndidzalemekeza mau ake.

11Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa;

munthu adzandichitanji?

12Zowindira Inu Mulungu, zili pa ine,

ndidzakuchitirani zoyamika.

13 Mas. 116.8 Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa,

simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe?

Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu

m'kuunika kwa amoyo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help