1 AKORINTO Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014
Mau Oyamba Kalata yoyamba ya Paulo kwa Akorinto inalembedwa pofuna kukonza mavuto okhudzana ndi moyo wachikhristu komanso chikhulupiriro amene anabuka mu mpingo umene Paulo anakhazikitsa ku Korinto. Mu nthawi imeneyo, unali mzinda waukulu Wachigriki wa malonda, ndipo unali likulu la dera la Akaya. Mzindawu umadziwika ndi malonda osiyanasiyana, miyambo yake yosiririka, za dama ndi zipembedzo zosiyanasiyana.Nkhawa yaikulu ya mtumwi inali mavuto amene analipo, monga kugawikana ndi chigololo komanso mafunso okhudzana ndi kugonana ndi banja, chikumbumtima, dongosolo la mu mpingo, mphatso za Mzimu Woyera ndi kuuka kwa akufa. Paulo akugwiritsa ntchito Uthenga Wabwino pofuna kufotokozera zonsezi bwino lomwe.Mu mutu 13, pamene akukamba za chikondi ngati mphatso ya mtengo wapatali ya Mulungu kwa anthu ake. Imeneyi ndi ndime yodziwika bwino mu bukuli.Za mkatimuMau oyamba 1.1-9Kugawana mu mpingo 1.10—4.21Za moyo wabanja ndikugonana koyenera 5.1—7.40Akhristu ndi akunja 8.1—11.1Moyo ndi chipembedzo cha mu mpingo 11.2—14.40Kuukanso kwa Yesu ndi kwa okhulupirira 15.1-58Chopereka cha akhristu a ku Yudeya 16.1-4Malonje ndi mau omaliza 16.5-24