AROMA 9 - Buku Lopatulika Bible 2014

Paulo alirira kusamvera kwa Israele

1Ndinena zoona mwa Khristu, sindinama ai, chikumbu mtima changa chichita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,

2Ulamuliro wa Mulungu wakusankha ena

6 Yoh. 8.39 Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala chabe ai. Pakuti onse akuchokera kwa Israele siali Israele;

7Gen. 21.12; Yoh. 8.39kapena chifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isaki, mbeu yako idzaitanidwa.

8Agal. 4.23, 28Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yake.

9Gen. 18.10, 14Pakuti mau a lonjezo ndi amenewa, Pa nyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana.

10Gen. 25.21Ndipo si chotero chokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isaki;

11Aro. 8.28pakuti anawo asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ai, koma chifukwa cha wakuitanayo,

12Gen. 25.23chotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.

13 Mala. 1.2-3 Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.

14 Deut. 32.4 Ndipo tsono tidzatani? Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ai.

15Eks. 33.19Pakuti anati ndi Mose, Ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni.

16Chotero sichifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo.

17Eks. 9.16Pakuti lembo linena kwa Farao, Chifukwa cha ichi, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi.

18Chotero Iye achitira chifundo amene Iye afuna, ndipo amene Iye afuna amuumitsa mtima.

19Pamenepo udzanena ndine kodi, Adandaulabe bwanji? Pakuti ndani anakaniza chifuno chake?

20Yes. 29.16Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero?

21Yer. 18.6Kodi kapena woumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuumba ndi nchinchi yomweyo chotengera chimodzi chaulemu ndi china chamanyazi?

22Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chionongeko?

23Aef. 1.7Ndi kuti Iye akadziwitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene Iye anazikonzeratu kuulemerero,

24Aro. 3.29ndi ife amenenso Iye anatiitana, si a mwa Ayuda okhaokha, komanso a mwa anthu amitundu?

25Hos. 2.23Monga atinso mwa Hoseya,

Amene sanakhala anthu anga, ndidzawatcha anthu anga;

ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.

26 Hos. 1.10 Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kunanenedwa kwa iwo,

Simuli anthu anga ai,

pomwepo iwo adzatchedwa ana a Mulungu wamoyo.

27 Yes. 1.9; 10.22-23; Aro. 11.5 Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti,

Ungakhale unyinji wa ana a Israele

ukhala monga mchenga wa kunyanja,

chotsalira ndicho chidzapulumuka.

28Pakuti Ambuye adzachita mau ake pa dziko lapansi, kuwatsiriza mwachidule.

29Yes. 1.9Ndipo monga Yesaya anati kale,

Ngati Ambuye wa makamu a kumwamba sanatisiyira ife mbeu,

tikadakhala monga Sodomu, ndipo tikadafanana ndi Gomora.

30 Aro. 10.20 Chifukwa chake tidzatani? Kuti amitundu amene sanatsata chilungamo, anafikira chilungamo, ndicho chilungamo cha chikhulupiriro;

31Aro. 10.2-3koma Israele, potsata lamulo la chilungamo, sanafikila lamulolo.

32Luk. 2.14; 1Ako. 1.23Chifukwa chanji? Chifukwa kuti sanachitsata ndi chikhulupiriro, koma monga ngati ndi ntchito. Anakhumudwa pa mwala wokhumudwitsa;

33Mas. 118.22; Mat. 21.42; Aro. 10.11monganso kwalembedwa, kuti,

Onani, ndikhazika m'Ziyoni mwala wakukhumudwa nao,

ndi thanthwe lophunthwitsa;

ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help