YESAYA 26 - Buku Lopatulika Bible 2014

Nyimbo yakulemekeza kutchinjiriza kwa Yehova

1 Yes. 60.18 Tsiku limenelo adzaimba nyimbo imeneyi m'dziko la Yuda, Ife tili ndi mudzi wolimba; Iye adzaika chipulumutso chikhale machemba ndi malinga.

2Mas. 118.19-20Tsegulani pazipata, kuti mtundu wolungama, umene uchita zoonadi, ulowemo.

3Yes. 30.15Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu.

4Deut. 32.4Khulupirirani Yehova nthawi yamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.

52Maf. 19.28Chifukwa Iye watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mudzi wa pamsanje; Iye wautsitsa, wautsitsira pansi; waugwetsa pansi pa fumbi.

6Phazi lidzaupondereza pansi; ngakhale mapazi a aumphawi, ndi mapondedwe a osowa.

7Mas. 37.23Njira ya wolungama ili njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama.

8Yes. 64.5Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu.

9Mas. 63.6Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.

10Aro. 2.4-5Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.

11Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.

12Mik. 5.4-5Yehova, mudzatikhazikitsira mtendere; pakuti mwatigwirira ntchito zathu zonse.

13Yehova Mulungu wathu, pamodzi ndi Inu Ambuye ena adatilamulira ife; koma mwa Inu nokha tidzatchula dzina lanu.

14Iwo afa, atha, sadzakhalanso ndi moyo; ali mizimu, sadzauka; chifukwa chake Inu munawazonda, ndi kuwaononga, mwathetsa chikumbukiro chao chonse.

15Mwachulukitsa mtundu, Yehova, mwachulukitsa mtundu; Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko.

16 Hos. 5.15 Yehova, iwo adza kwa Inu movutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.

17Yoh. 16.21Monga ngati mkazi wokhala ndi pakati, amene nthawi yake yakubala yayandikira, amva zopweteka, ndi kufuula m'zowawa zake; momwemo takhala ife pamaso panu, Yehova.

18Ife tinali ndi pakati, ife tinamva zopweteka, tafanana ngati tabala mphepo; sitinachite chipulumutso chilichonse pa dziko lapansi; ngakhale okhala m'dziko lapansi sanagwe.

19Ezk. 37; Dan. 12.2Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.

20 Eks. 12.22-23 Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.

21Mik. 1.3; Yud. 14Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera kumalo ake kudzazonda okhala pa dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help