1
3likumbukire zopereka zako zonse,
lilandire nsembe yako yopsereza;
4 Mas. 21.2 likupatse cha mtima wako,
ndipo likwaniritse upo wako wonse.
5 Mas. 9.14; 60.4 Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu,
ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera;
Yehova akwaniritse mapempho ako onse.
6Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wake;
adzamvomereza m'Mwamba mwake moyera
ndi mphamvu ya chipulumutso cha dzanja lake lamanja.
7 2Mbi. 32.8; Mas. 33.16-17; Miy. 21.31 Ena atama magaleta, ndi ena akavalo;
koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.
8Iwowa anagonjeka, nagwa;
koma ife tauka, ndipo takhala chilili.
9Yehova, pulumutsani,
mfumuyo ativomereze tsiku lakuitana ife.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.