1 Chiv. 1.18 Ndipo ndinaona mngelo anatsika Kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha ku chiphompho chakuya, ndi unyolo waukulu m'dzanja lake.
22Pet. 2.4Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi,
3Chiv. 20.8namponya ku chiphompho chakuya, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthawi.
4Mat. 19.28; Aro. 8.17; 2Tim. 2.12; Chiv. 6.9Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira chilombo, kapena fano lake, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.
5Otsala a akufa sanakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka chikwi. Ndiko kuuka kwa akufa koyamba.
6Chiv. 2.11; 21.8Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiwiri ilibe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo.
Satana amasulidwa naonongeka7 Chiv. 20.2 Ndipo pamene zidzatha zaka chikwi, adzamasulidwa Satana m'ndende yake;
8Ezk. 38.2; Chiv. 16.14; 20.3, 10nadzatuluka kudzasokeretsa amitundu ali mungodya zinai za dziko, Gogi, ndi Magogi, kudzawasonkhanitsa achite nkhondo: chiwerengero chao cha iwo amene chikhala ngati mchenga wa kunyanja.
9Ezk. 38.9, 16Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo: ndipo unatsika moto wakumwamba nuwanyeketsa.
10Chiv. 19.20Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulufure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.
Chiweruziro chotsiriza11 2Pet. 3.7, 10-11 Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwa malo ao.
12Yer. 17.10; Dan. 7.10; Mat. 16.27; 2Ako. 5.10; Afi. 4.3; Chiv. 21.27Ndipo ndinaona akufa, akulu ndi ang'ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa ntchito zao.
13Yer. 17.10; Mat. 16.27; 2Ako. 5.10; Chiv. 6.8Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi dziko la akufa zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake.
141Ako. 15.26, 54-55; Chiv. 20.6Ndipo imfa ndi dziko la akufa zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto.
15Chiv. 19.20Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.