YONA Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014

Mau OyambaBuku la Yona likusiyana ndi mabuku ena a aneneri a mu Baibulo chifukwa likufotokoza mwatsatanetsatane zimene adachita mneneriyo amene sadafune kumvera lamulo la Mulungu. Mulungu anamuuza kuti apite kumzinda wa Ninive, umene unali likulu ka ufumu wamphamvu wa Asiriya, amene anali mdani woipitsitsa wa Aisraele. Koma Yona sanafune kukalalikira uthenga wa Mulungu kumeneko, chifukwa amakhulupirira kuti Mulunguyo sakaononga mzindawo. Patachitika zinthu zingapo zodabwitsa, iyeyo anavomera ndipo pa mapeto ake anakwiya ataona kuti uthenga wake wa chilango sunapherezere.Bukuli likuonetsa kuti Mulungu ali ndi ulamuliro wonse pa chilengedwe. Komanso likuonetsa kuti Mulungu ndi wachikondi ndi wachifundo, amene amafunitsitsa kukhululukira ndi kupulumutsa adani a anthu ake ngati alapa, osati ndi kuwalanga kapena kuwaononga.Za mkatimuKuitanidwa kwa Yona ndi kusamvera kwake 1.1-17

Yona alapa napulumutsidwa 2.1-10

Uthenga wa Yona wotsutsana ndi Ninive 3.1-10

Chifundo cha Mulungu pa Ninive 4.1-11

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help