1Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova masiku a Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kuti,
21Maf. 6.5Pita kunyumba ya Arekabu, nunene nao, nulowetse iwo m'nyumba ya Yehova, m'chipinda china, nuwapatse iwo vinyo amwe.
3Ndipo ndinatenga Yazaniya mwana wa Yeremiya, mwana wa Habaziniya, ndi abale ake, ndi ana amuna ake, ndi nyumba yonse ya Arekabu;
4ndipo ndinawalowetsa m'nyumba ya Yehova, m'chipinda cha ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu, chokhala pambali pa chipinda cha akulu, ndicho chosanjika pa chipinda cha Maaseiya mwana wa Salumu, mdindo wa pakhomo;
5ndipo ndinaika pamaso pa ana amuna a nyumba ya Arekabu mbale zodzala ndi vinyo, ndi zikho, ndipo ndinati kwa iwo, Imwani vinyo.
6Lev. 10.9; Num. 6.1-4; 2Maf. 10.15; Dan. 1.8Koma anati, Sitidzamwa vinyo; pakuti Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu anatiuza ife, kuti, Musadzamwe vinyo, kapena inu, kapena ana anu, kumuyaya;
7ndiponso musamange nyumba, musafese mbeu, musaoke mipesa, musakhale nayo; koma masiku anu onse mudzakhale m'mahema; kuti mukhale ndi moyo masiku ambiri m'dziko limene mukhalamo alendo.
8Ndipo ife tamva mau a Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu m'zonse zimene anatiuza ife, zakuti tisamwe vinyo masiku athu onse, ife, akazi athu, ana athu aamuna ndi aakazi;
9ngakhale kudzimangira nyumba zokhalamo; ndipo sitili nao munda wamphesa, kapena munda, kapena mbeu;
10koma takhala m'mahema, ntimvera, ntichita monga mwa zonse anatiuza Yonadabu kholo lathu.
11Koma panali, pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anadza m'dzikomu, ife tinati, Tiyeni tinke ku Yerusalemu chifukwa tiopa nkhondo ya Ababiloni, ndi nkhondo ya Aramu; ndipo tikhala m'Yerusalemu.
12Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,
13Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Pita, nunene kwa anthu a Yuda ndi kwa okhala m'Yerusalemu, Kodi simudzalola kulangizidwa kumvera mau anga? Ati Yehova.
14Yer. 35.6Mau a Yonadabu mwana wa Rekabu, amene anauza ana ake, asamwe vinyo, alikuchitidwa, ndipo mpaka lero samamwa, pakuti amvera lamulo la kholo lao; koma Ine ndanena ndi inu, ndalawirira ndi kunena; koma simunandimvera Ine.
152Maf. 17.13Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yake yoipa, konzani machitidwe anu, musatsate milungu ina kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunanditchera khutu lanu, simunandimvera Ine.
16Pakuti monga ana a Yonadabu mwana wa Rekabu achita lamulo la kholo lao limene anawauza, koma anthu awa sanandimvere Ine.
17Miy. 1.24Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzafikitsa pa Yuda ndi pa onse okhala m'Yerusalemu choipa chonsecho ndawanenera iwo; chifukwa ndanena ndi iwo, koma sanamve; ndaitana, koma iwo sanandivomere.
18Ndipo Yeremiya anati kwa nyumba ya Arekabu, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa mwamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndi kusunga zonse anakulangizani inu, ndi kuchita monga mwa zonse anakuuzani inu;
19chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Yonadabu mwana wa Rekabu sadzasowa munthu wakuima pamaso panga kumuyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.