1Ndipo Yehova anati kwa Mose, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja; ndipo ndidzalembera pa magomewo mau omwewo anali pa magome oyambawo, amene unawaswa.
2Nukonzekeretu m'mawa, nukwere m'mawa m'phiri la Sinai, nuimepo pamaso panga pamwamba pa phiri.
3Palibe munthu akwere ndi iwe, asaonekenso munthu aliyense m'phiri monse; ndi zoweta zazing'ono kapena zoweta zazikulu zisadye kuphiri kuno.
4Ndipo anasema magome awiri a miyala, onga oyamba aja; ndipo Mose anauka mamawa nakwera m'phiri la Sinai, monga Yehova adamuuza, nagwira m'dzanja mwake magome awiri amiyala.
5Ndipo Yehova anatsika mumtambo, naimapo pamodzi ndi iye, nafuula dzina la Yehova.
6Mas. 86.15Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi;
7Mas. 103.3; 145.8; Yer. 32.18wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulangira ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
8Ndipo Mose anafulumira, naweramira pansi nalambira.
9Mas. 33.12; 94.14; Zek. 2.12Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopano pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi uchimo wathu, ndipo mutilandire tikhale cholowa chanu.
10Deut. 5.2Ndipo Iye anati, Taona, Ine ndichita pangano; ndidzachita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinachitika zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uliwonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona ntchito ya Yehova, pakuti chinthu ndikuchitirachi nchoopsa.
11Dzisungire chimene Ine ndikuuza lero lino: taona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.
12Ower. 2.2Dzichenjere ungachite pangano ndi anthu a ku dziko limene umukako, lingakhale msampha pakati panu;
13koma mupasule maguwa a nsembe ao, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao;
14Eks. 20.5pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;
15ungachite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angachite chigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zake;
161Maf. 11.1, 2; Ezr. 9.2ndipo ungatengereko ana ako amuna ana ao akazi; nangachite chigololo ana ao akazi potsata milungu yao, ndi kuchititsa ana anu amuna chigololo potsata milungu yao.
17Usadzipangire milungu yoyenga.
18Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka m'Ejipito.
19Eks. 13.2, 12Onse oyambira kubadwa ndi anga; ndi zoweta zanu zonse zazimuna, zoyamba za ng'ombe ndi za nkhosa.
20Eks. 23.15Koma woyamba wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu amuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu.
21Eks. 20.9Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito, koma lachisanu ndi chiwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula.
22Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.
23Amuna ako onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, katatu chaka chimodzi.
24Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu chaka chimodzi.
25Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi nsembe yophera ya chikondwerero cha Paska asaisiye kufikira m'mawa.
26Uzibwera nazo zipatso zoyambayamba za nthaka yako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.
27Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israele.
28Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadye mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.
Nkhope ya Mose inyezimira29 2Ako. 3.7, 13; Mat. 17.2 Ndipo kunali pakutsika Mose pa phiri la Sinai, ndi magome awiri a mboni m'dzanja lake la Mose, pakutsika iye m'phirimo, Mose sanadziwe kuti khungu la nkhope yake linanyezimira popeza Iye adalankhula naye.
30Ndipo pamene Aroni ndi ana onse a Israele anaona Mose, taonani, khungu la nkhope yake linanyezimira; ndipo anaopa kumyandikiza.
31Koma Mose anawaitana; ndipo Aroni ndi akazembe onse a khamu la anthu anabwera kwa iye; ndipo Mose analankhula nao.
32Ndipo atatero, ana onse a Israele anayandikiza; ndipo iye anawauza zonse Yehova adalankhula naye m'phiri la Sinai.
332Ako. 3.7, 13Ndipo Mose atatha kulankhula nao, anaika chophimba pankhope pake.
342Ako. 3.16Koma pakulowa Mose pamaso pa Yehova kunena ndi Iye, anachotsa chophimbacho, kufikira akatuluka; ndipo atatuluka analankhula ndi ana a Israele chimene adamuuza.
35Ndipo ana a Israele anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso chophimba pankhope pake, kufikira akalowa kulankhula ndi Iye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.