1 Num. 36.1-11 Pamenepo anayandikiza ana akazi a Zelofehadi mwana wa Hefere, ndiye mwana wa Giliyadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ake akazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.
2Ndipo anaima pamaso pa Mose, ndi pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa akalonga; ndi khamu lonse, pakhomo pa chihema chokomanako, ndi kuti,
3Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana amuna.
4Lichotsedwerenji dzina la atate wathu pakati pa banja lake, popeza alibe mwana wamwamuna? Tipatseni dziko lathulathu pakati pa abale a atate wathu.
5Ndipo Mose anapita nao mlandu wao pamaso pa Yehova.
6Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
7Ana akazi a Zelofehadi anena zoona; uwapatse ndithu cholowa chikhale chaochao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse cholowa cha atate wao.
8Ndipo unene ndi ana a Israele, ndi kuti, Akafa munthu wamwamuna wopanda mwana wamwamuna, cholowa chake achilandire mwana wake wamkazi.
9Ndipo akapanda kukhala naye mwana wamkazi, mupatse abale ake cholowa chake.
10Ndipo akapanda kukhala nao abale, mupatse abale a atate wake cholowa chake.
11Ndipo akapanda abale a atate wake, mupatse wa chibale chake woyandikizana naye wa fuko lake cholowa chake, likhale lakelake; ndipo likhale kwa ana a Israele lemba monga Yehova wamuuza Mose.
Aikidwa Yoswa m'malo mwa Mose12Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kwera m'phiri ili la Abarimu, nupenye dziko limene ndapatsa ana a Israele.
13Utaliona iwenso udzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wako, monga anaitanidwa Aroni mbale wako;
14Num. 20.12, 24popeza munapikisana nao mau anga m'chipululu cha Zini, potsutsana nane khamulo, osandipatula Ine pa madziwo pamaso pao. Ndiwo madzi a Meriba m'Kadesi, m'chipululu cha Zini.
15Ndipo Mose ananena ndi Yehova, nati,
16Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, aike munthu pa khamulo,
171Maf. 22.17; Mat. 9.36wakutuluka pamaso pao, ndi kulowa pamaso pao, wakuwatulutsa ndi kuwalowetsa; kuti khamu la Ambuye lisakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.
18Gen. 41.38; Deut. 34.9Ndipo Yehova anati kwa Mose, Utenge Yoswa mwana wa Nuni, ndiye munthu mwa iye muli mzimu, nuike dzanja lako pa iye;
19Deut. 31.7numuimike pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse; numlangize pamaso pao.
202Maf. 2.15Ndipo umuikirepo ulemerero wako, kuti khamu lonse la ana a Israele ammvere.
21Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa chiweruzo cha Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituluka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israele pamodzi naye, ndiwo khamu lonse.
22Ndipo Mose anachita monga Yehova adamuuza; natenga Yoswa namuimitsa pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse;
23Num. 27.19namuikira manja ake, namlangiza monga Yehova adanena ndi dzanja la Mose.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.