1Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chiwiri, munali chete m'Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka.
2Mat. 18.10Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.
3 Chiv. 5.8 Ndipo anadza mngelo wina, naima pa guwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse pa guwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu.
4Mas. 141.2Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kutuluka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.
5Chiv. 16.18Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi moto wopala pa guwa la nsembe, nauponya pa dziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi chivomezi.
6Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nao malipenga anadzikonzera kuti aombe.
7 Ezk. 38.22 Ndipo woyamba anaomba lipenga, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosanganiza ndi mwazi, ndipo anazitaya pa dziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.
8 Amo. 7.4 Ndipo mngelo wachiwiri anaomba lipenga, ndipo monga ngati phiri lalikulu lakupserera ndi moto linaponyedwa m'nyanja; ndipo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka mwazi;
9Chiv. 16.3ndipo lidafa limodzi la magawo atatu a zolengedwa zili m'nyanja, zokhala ndi moyo; ndipo limodzi la magawo atatu a zombo lidaonongeka.
10 Yes. 14.12 Ndipo mngelo wachitatu anaomba lipenga, ndipo idagwa kuchokera kumwamba nyenyezi yaikulu, yoyaka ngati muuni, ndipo idagwa pa limodzi la magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe amadzi;
11Eks. 15.23; Rut. 1.20ndipo dzina lake la nyenyeziwo alitcha Chowawa; ndipo limodzi la magawo atatu a madzi lidasanduka chowawa; ndipo anthu ambiri adafa pakumwa madzi, pakuti asananduka owawa.
12 Yes. 13.10 Ndipo mngelo wachinai anaomba lipenga, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ake atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo.
13 Chiv. 9.12 Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pa mwamba, ndi kunena ndi mau akulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.