1 AKORINTO 14 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mphatso ya kunenera iposa ya malilime

1 1Ako. 12.31 Tsatani chikondi; koma funitsitsani mphatso zauzimu, koma koposa kuti mukanenere.

2Mac. 10.46Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.

3Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu chomangirira ndi cholimbikitsa, ndi chosangalatsa.

4Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangirira Mpingo.

5Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira.

61Ako. 14.26Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikakupindulitsani chiyani, ngati sindilankhula ndi inu kapena m'vumbulutso, kapena m'chidziwitso, kapena m'chinenero, kapena m'chiphunzitso?

7Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati chitoliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, chidzazindikirika bwanji chimene chiombedwa kapena kuimbidwa?

8Pakuti ngati lipenga lipereka mau osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?

9Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mau omveka bwino, kudzazindikirika bwanji chimene chilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga.

10Ilipo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau pa dziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau.

11Chifukwa chake, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwa ine.

12Momwemo inunso, popeza muli ofunitsitsa mphatso za Mzimu, funani kuti mukachuluke kukumangirira kwa Mpingo.

13Chifukwa chake wolankhula lilime, apemphere kuti amasule.

14Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa chikhala chosabala kanthu.

15Mas. 47.7; Aef. 5.19Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso.

16Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena?

17Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwa.

18Ndiyamika Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse;

19koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi zidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime.

20 Aro. 16.19 Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu.

21Yes. 28.11-12Kwalembedwa m'chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.

22Chotero malilime akhala ngati chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira, koma kwa iwo osakhulupirira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira.

23Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mwayaluka?

24Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;

25Zek. 8.23zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.

Chipembedzo chichitike molongosoka

26 2Ako. 12.19 Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira.

27Ngati wina alankhula lilime, achite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire.

28Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.

29Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire.

30Koma ngati kanthu kuvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale chete woyambayo.

31Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzimmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe;

32ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri;

33pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.

34 1Tim. 2.11-12; Akol. 3.18 Akazi akhale chete m'Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena.

35Koma ngati afuna kuphunzira kanthu afunse amuna ao a iwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo.

36Kodi mau a Mulungu anatuluka kwa inu? Kapena anafika kwa inu nokha?

37 2Ako. 10.7 Ngati wina ayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye.

38Koma ngati wina akhale wosadziwa, akhale wosadziwa.

39 1Ate. 5.20 Chifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime.

401Ako. 14.33Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help