LEVITIKO 8 - Buku Lopatulika Bible 2014

Kupatulidwa kwa ansembe

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;

3nusonkhanitse khamu lonse ku khomo la chihema chokomanako.

4Ndipo Mose anachita monga Yehova anamuuza; ndi khamulo linasonkhana pa khomo la chihema chokomanako.

5Ndipo Mose anati kwa msonkhanowo, Ichi ndi chimene Yehova adauza kuti chichitike.

6Ndipo Mose anabwera nao Aroni ndi ana ake, nawasambitsa ndi madzi.

7Ndipo anamveka ndi malaya a m'kati, nammanga m'chuuno ndi mpango, namveka ndi mwinjiro, namveka ndi efodi, nammanga m'chuuno ndi mpango wa efodi nammanga nao pathupi pake.

8Ndipo anamuika chapachifuwa; naika m'chapachifuwa Urimu ndi Tumimu.

9Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.

10Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza Kachisi, ndi zonse zili m'mwemo, nazipatula.

11Ndipo anawazako pa guwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake, kuzipatula.

12Mas. 133.2Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula.

13Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawaveka malaya a m'kati, nawamanga m'chuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adzauza Mose.

14Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pa mutu wa ng'ombe ya nsembe yauchimo.

15Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi chala chake pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde pa guwa la nsembe, nalipatula, kuti alichitire cholitetezera.

16Ndipo anatenga mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndipo Mose anazitentha pa guwa la nsembe.

17Koma ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi nyama yake, ndi chipwidza chake, anazitentha ndi moto kunja kwa chigono; monga Yehova adamuuza Mose.

18Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo.

19Ndipo anaipha; ndi Mose anawaza mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira.

20Ndipo anapadzula mphongoyo ziwalo zake; ndi Mose anatentha mutuwo ndi ziwalo, ndi mafuta.

21Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

Kupatulidwa kwa Aroni ndi ana ake

22Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pa mutu wa mphongoyo.

23Ndipo anaipha; ndi Mose anatengako mwazi wake naupaka pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lake, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja.

24Pamenepo anabwera nao ana amuna a Aroni, ndi Mose anatengako mwazi, naupaka pa ndewerere ya khutu lao la ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lao, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao la ku dzanja lamanja; ndipo Mose anawaza mwaziwo pa guwa la nsembe pozungulira.

25Ndipo anatenga mafutawo ndi mchira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;

26ndipo mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova, anatengeramo kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa, ndi kamtanda kamodzi ka mkate wamafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, natiika pa mafutawo, ndi pa mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;

27anaika zonsezi m'manja mwa Aroni, ndi m'manja mwa ana ake amuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

28Pamenepo Mose anazichotsa ku manja ao, nazitentha pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza; ndizo nsembe zodzaza manja zochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.

29Ndipo Mose anatenga ngangayo naiweyula, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndilo gawo la Mose la ku nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; monga Yehova adamuuza Mose.

30Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala pa guwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake amuna, ndi pa zovala za ana ake amuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake amuna, ndi zovala za ana ake amuna omwe.

31Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ake amuna, Phikani nyamayi pakhomo pa chihema chokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu dengu la nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ake aidye.

32Koma chotsalira cha nyama ndi mkate muchitenthe ndi moto.

33Ndipo musatuluka pa khomo la chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, kufikira anakwanira masiku a kudzaza manja kwanu; pakuti adzaze manja anu masiku asanu ndi awiri.

34Monga anachita lero lino, momwemo Yehova anauza kuchita, kukuchitirani chotetezera.

35Zek. 3.7Ndipo mukhale pakhomo pa chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku, ndi kusunga chilangizo cha Yehova, kuti mungafe; pakuti anandiuza kotero.

36Ndipo Aroni ndi ana ake amuna anachita zonse zimene Yehova anauza pa dzanja la Mose.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help