YOSWA 4 - Buku Lopatulika Bible 2014

Aimiritsa miyala 12 ikhale chikumbutso ku Giligala

1Ndipo kunali, utatha kuoloka Yordani mtundu wonse, Yehova ananena ndi Yoswa, nati,

2Mudzitengere mwa anthu, amuna khumi ndi awiri, fuko limodzi mwamuna mmodzi;

3Deut. 27.2, 19-20ndipo muwalamulire iwo ndi kuti, Mudzitengere pano pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe, miyala khumi ndi iwiri, ndi kuoloka nayo, ndi kuiika m'mogona m'mene mugonamo usiku uno.

4Pamenepo Yoswa anaitana amuna khumi ndi awiriwo amene anawaikiratu mwa ana a Israele, fuko limodzi mwamuna mmodzi;

5nanena nao Yoswa, Olokani, kutsogolera likasa la Yehova Mulungu wanu pakati pa Yordani, nimudzisenzere yense mwala paphewa pake, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele;

6Mas. 44.1kuti ichi chikhale chizindikiro pakati pa inu. Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani ndi inu?

7Eks. 12.14; Yos. 3.13, 16Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo pa likasa la chipangano cha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire.

8Ndipo ana a Israele anachita monga Yoswa anawalamulira, nasenza miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, monga Yehova adalankhula ndi Yoswa, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele; ndipo anaoloka nayo kunka kogona, naiika komweko.

9Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la chipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.

10Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordani, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.

11Ndipo kunali, atatha kuoloka anthu onse, likasa la Yehova linaoloka, ndi ansembe, pamaso pa anthu.

12Num. 32.20, 27-28Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi gawo lija la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao;

13ngati zikwi makumi anai ankhondo okonzeka anaoloka pamaso pa Yehova kuthira nkhondo ku zidikha za Yeriko.

14Yos. 3.7Tsiku lomwelo Yehova anakulitsa Yoswa pamaso pa Aisraele onse; ndipo anamuopa monga anaopa Mose, masiku onse a moyo wake.

15Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,

16Lamulira ansembe akusenza likasa la umboni, kuti akwere kutuluka m'Yordani.

17Pamenepo Yoswa analamulira ansembe, ndi kuti, Kwerani kutuluka m'Yordani.

18Yos. 3.15Ndipo kunali, atakwera ansembe akusenza likasa la chipangano la Yehova, kutuluka pakati pa Yordani, nakwera pamtunda mapazi a ansembe, madzi a m'Yordani anabwera m'njira mwake, nasefuka m'magombe ake onse monga kale.

19Ndipo anthu anakwera kutuluka m'Yordani tsiku lakhumi la mwezi woyamba, namanga misasa ku Giligala, mbali ya ku m'mawa kwa Yeriko.

20Yos. 4.3Ndipo Yoswa anaimika ku Giligala miyala ija khumi ndi iwiri adaitenga m'Yordani.

21Yos. 4.6Ndipo anati kwa ana a Israele, Ana anu akadzafunsa atate ao masiku akudza, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani?

22Pamenepo muzidziwitsa ana anu, ndi kuti, Israele anaoloka Yordani uyu pouma.

23Eks. 14.21-22Pakuti Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yordani pamaso panu, mpaka mutaoloka; monga Yehova Mulungu wanu anachitira Nyanja Yofiira, imene anaiphwetsa pamaso pathu, mpaka titaoloka;

241Maf. 8.42-43; 2Maf. 19.19; Yer. 10.7kuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi idziwe dzanja la Yehova, kuti ndilo lamphamvu; kuti iope Yehova Mulungu wanu masiku onse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help