1 Deut. 24.1; Yes. 52.3; Yer. 3.8; Mat. 18.25 Atero Yehova, Kalata wa chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.
2Eks. 14.21; Yes. 59.1Chifukwa chanji ndinafika osapeza munthu? Ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? Pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndi kusandutsa mitsinje chipululu; nsomba zake zinunkha chifukwa mulibe madzi, nizifa ndi ludzu.
3Eks. 10.21Ndiveka thambo ndi kuda, ndi kuyesa chiguduli chofunda chake.
4 Eks. 4.11; Mat. 11.28 Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.
5Yoh. 14.31; Afi. 2.8Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhala wopanduka ngakhale kubwerera m'mbuyo.
6Mat. 26.7; 27.26Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisira nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.
7Ezk. 3.8-9; Luk. 9.51Pakuti Ambuye Yehova adzandithangata Ine; chifukwa chake sindinasokonezedwa; chifukwa chake ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndidziwa kuti sindidzakhala ndi manyazi.
8Aro. 8.32-34Iye ali pafupi amene alungamitsa Ine; ndani adzakangana ndi Ine? Tiyeni tiimirire tonse pamodzi; mdani wanga ndani? Andiyandikire.
9Mas. 102.26-28; Yes. 51.6, 8Taonani, Ambuye Yehova adzathandiza Ine; ndani amene adzanditsutsa? Taonani, iwo onse adzatha ngati chovala, njenjete zidzawadya.
10 Mas. 23.4 Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.
11Taonani, inu nonse amene muyatsa moto, amene mudzimangira m'chuuno ndi nsakali, yendani inu m'chilangali cha moto wanu, ndi pakati pa nsakali zimene mwaziyatsa. Ichi mudzakhala nacho cha pa dzanja langa; mudzagona pansi ndi chisoni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.