1Mau amene anadza kwa Yeremiya za anthu onse a Yuda chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda; ndicho chaka choyamba cha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni;
2amene mneneri Yeremiya ananena kwa anthu onse a Yuda, ndi onse okhala m'Yerusalemu, kuti:
3Yer. 7.13Kuyambira chaka chakhumi ndi chitatu cha Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Yuda, kufikira lero lomwe, zakazi makumi awiri ndi zitatu, mau a Yehova anafika kwa ine, ndipo ndanena kwa inu, pouka mamawa ndi kunena; koma simunamvera.
4Ndipo Yehova watuma kwa inu atumiki ake onse ndiwo aneneri, pouka mamawa ndi kuwatuma; koma simunamvera, simunatchera khutu lanu kuti mumve;
52Maf. 17.13ndi kuti, Mubwerere tsopano nonsenu, yense kuleka njira yake yoipa, ndi zoipa za ntchito zanu, ndi kukhala m'dziko limene Yehova anapatsa inu ndi makolo anu, kuyambira kale kufikira muyaya;
6musatsate milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, musautse mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu; ndingachitire inu choipa.
7Deut. 32.21Koma simunandimvera Ine, ati Yehova; kuti muutse mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu ndi kuonapo choipa inu.
8Chifukwa chake Yehova wa makamu atero: Popeza simunamvera mau anga,
9Yer. 1.15taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo pa dziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.
10Ezk. 26.13Ndiponso ndidzawachotsera mau akusekera ndi mau akukondwera, ndi mau a mkwati, ndi mau a mkwatibwi, mau a mphero, ndi kuwala kwa nyali.
11Ndipo dziko lonseli lidzakhala labwinja, ndi chizizwitso, ndipo mitundu iyi idzatumikira mfumu ya ku Babiloni zaka makumi asanu ndi awiri.
122Mbi. 36.21-22Ndipo kudzakhala, zitapita zaka makumi asanu ndi awiri, ndidzalanga mfumu ya ku Babiloni, ndi mtundu uja womwe, ati Yehova, chifukwa cha mphulupulu zao, ndi dziko la Ababiloni; ndipo ndidzaliyesa mabwinja amuyaya.
13Ndipo ndidzatengera dzikolo mau anga onse amene ndinanenera ilo, mau onse olembedwa m'buku ili, amene Yeremiya wanenera mitundu yonse.
14Pakuti mitundu yambiri ndi mafumu akulu adzayesa iwo atumiki ao; ndipo ndidzabwezera iwo monga mwa machitidwe ao, monga mwa ntchito ya manja ao.
15 Chiv. 14.10 Pakuti Yehova, Mulungu wa Israele, atero kwa ine, Tenga chikho cha vinyo wa ukaliwu pa dzanja langa, ndi kumwetsa mitundu yonse, imene ndikutumizirako.
16Ndipo adzamwa, nadzayenda dzandidzandi, nadzachita misala, chifukwa cha lupanga limene Ine ndidzatumiza mwa iwo.
17Ndipo ndinatenga chikho pa dzanja la Yehova, ndinamwetsa mitundu yonse, imene Yehova ananditumizirako;
18Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, ndi mafumu ake omwe, ndi akulu ake, kuwayesa iwo bwinja, chizizwitso, chotsonyetsa, ndi chitemberero; monga lero lino;
19Yer. 46
Farao mfumu ya ku Ejipito, ndi atumiki ake, ndi akulu ake, ndi anthu ake onse;20Yer. 47ndi anthu onse osanganizidwa, ndi mafumu onse a dziko la Uzi, ndi mafumu onse a dziko la Afilisti, ndi Asikeloni, ndi Gaza, ndi Ekeroni, ndi otsala a Asidodi,
21Edomu, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni,
22ndi mafumu onse a Tiro, ndi mafumu onse a Sidoni, ndi mafumu a chisumbu chimene chili patsidya pa nyanja;
23Dedani, ndi Tema, ndi Buzi, ndi onse amene ameta m'mbali mwa tsitsi;
24ndi amfumu onse a Arabiya, ndi mafumu onse a anthu osanganizidwa okhala m'chipululu;
25ndi mafumu onse a Zimiri, ndi mafumu onse a Elamu, ndi mafumu onse a ku Mediya,
26ndi mafumu onse a kumpoto, a kutali ndi a kufupi, wina ndi mnzake; ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala pansi pano; ndi mfumu ya Sesaki adzamwa pambuyo pao.
27Ndipo uziti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Imwani inu, ndi kuledzera, ndi kusanza, ndi kugwa, osanyamukanso konse, chifukwa cha lupanga limene ndidzatumiza mwa inu.
28Ndipo padzakhala, ngati akana kutenga chikho pa dzanja lako kuti amwe, uziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Kumwa muzimwa,
29Oba. 1.15-16Pakuti, taonani, ndiyamba kuchita choipa pa mudzi umene utchedwa ndi dzina langa, kodi inu mudzakhala osalangidwa konse? Simudzakhala osalangidwa; pakuti ndidzaitana lupanga ligwe pa onse okhala m'dziko lapansi, ati Yehova wa makamu.
30Yow. 3.16Chifukwa chake muwanenere iwo mau onse awa, ndi kuti kwa iwo, Yehova adzabangula kumwamba, nadzatchula mau ake mokhalamo mwake moyera; adzabangulitsira khola lake; adzafuula, monga iwo akuponda mphesa, adzafuulira onse okhala m'dziko lapansi.
31Hos. 4.1Phokoso lidzadza ku malekezero a dziko lapansi; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi mitundu ya anthu, adzatsutsana ndi anthu onse; koma oipa, adzawapereka kulupanga, ati Yehova.
32Yehova wa makamu atero, Taonani, zoipa zidzatuluka kumtundu kunka m'mitundu, ndipo namondwe adzauka kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
33Yes. 66.16Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dziko lapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.
34Yer. 23.1Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akulu a zoweta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati chotengera chofunika.
35Ndipo abusa adzasowa pothawira, mkulu wa zoweta adzasowa populumukira.
36Mau akufuula abusa, ndi kukuwa mkulu wa zoweta! Pakuti Yehova asakaza busa lao.
37Ndipo makola amtendere adzaonongeka chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.
38Wasiya ngaka yake, monga mkango; pakuti dziko lao lasanduka chizizwitso chifukwa cha ukali wa lupanga losautsa, ndi chifukwa cha mkwiyo wake waukali.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.