1 1Ako. 2.14-15 Ndipo ine, abale, sindinakhoza kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu.
2Aheb. 5.12-13Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ai; pakuti simunachikhoza; ngakhale tsopano lino simuchikhoza; pakuti mulinso athupi;
31Ako. 1.11pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?
41Ako. 1.12Pakuti pamene wina anena, Ine ndine wa Paulo; koma mnzake, Ndine wa Apolo; simuli anthu kodi?
51Ako. 4.1Ndipo Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa.
6Mac. 18.4, 8, 11, 24; 1Ako. 15.10Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa.
7Mac. 18.4, 8, 11, 24; 1Ako. 15.10Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.
8Aro. 2.6Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha.
Akhristu ali nyumba ya Mulungu, Yesu ali maziko a nyumbayi9 2Ako. 6.1; Aef. 2.20-22 Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.
10Aro. 15.20; 1Pet. 4.11Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo.
11Aro. 11.33-34Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Khristu.
12Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golide, siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, udzu, dziputu,
131Ako. 4.5ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.
141Ako. 4.5Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene anaimangako, adzalandira mphotho.
15Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto.
16 1Ako. 6.19 Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?
17Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.
18 Yes. 5.21 Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m'nthawi yino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru.
19Yes. 5.21Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao;
20Mas. 94.11ndiponso Ambuye azindikira zolingirira za anzeru, kuti zili zopanda pake.
212Ako. 4.15Chifukwa chake palibe mmodzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse nzanu;
22ngati Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena za makono ano, kapena zilinkudza; zonse ndi zanu;
23Aro. 14.8koma inu ndinu a Khristu; ndi Khristu ndiye wa Mulungu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.