1Ndifuula nalo liu langa kwa Yehova;
ndi mau anga ndipemba kwa Yehova.
2 Yes. 26.16 Nditsanulira kudandaula kwanga pamaso pake;
ndionetsa msauko wanga pamaso pake.
3 Mas. 141.9 Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga.
M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.
4 Mas. 31.11 Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa;
pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.
5 Mas. 46.1 Ndinafuulira kwa inu, Yehova;
ndinati, Inu ndinu pothawirapo panga,
gawo langa m'dziko la amoyo.
6 Mas. 116.6 Tamverani kufuula kwanga; popeza ndisauka kwambiri;
ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andilaka.
7Tulutsani moyo wanga m'ndende, kuti ndiyamike dzina lanu;
olungama adzandizinga;
pakuti mudzandichitira zokoma.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.