HAGAI Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014
Mau OyambaMneneriyu adalalika mau ake chaka cha 520 BC., Ayuda ena atabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo. Anthuwo anali atabwerera ku ukapolo namakhala ku Yerusalemu kwa zaka zingapo, koma Kachisi anali bwinja lenileni. Atsogoleri anapereka uthenga kwa anthu kuti amangenso Kachisi, ndipo Ambuye akulonjeza kuti m'tsogolo anthu ake adzakhala pabwino ndi pa mtendere.Za mkatimuYehova awalamula kuti amangenso Nyumba yake 1.1-15Mau ena owalimbitsa mtima Ayudawo 2.1-23