1 Mas. 24.3-5 Yehova, ndani adzagonera m'chihema mwanu?
Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika?
2 Yes. 33.15-16; Aef. 4.25 Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo,
nanena zoonadi mumtima mwake.
3 Lev. 19.16 Amene sasinjirira ndi lilime lake,
nachitira mnzake choipa,
ndipo satola miseche pa mnansi wake.
4 Ower. 11.35 M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka;
koma awachitira ulemu akuopa Yehova.
Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.
5 Lev. 25.36, 39; 2Pet. 1.10 Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu,
ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa.
Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.