HABAKUKU 2 - Buku Lopatulika Bible 2014

Ababiloni omwe adzalangidwa

1 Yes. 21.8; Mas. 85.8 Ndidzaima pa dindiro langa ndi kudziika palinga, ndipo ndidzayang'anira ndione ngati adzanenanji mwa ine, ngatinso ndidzamyankha chiyani pa choneneza changa.

2Ndipo Yehova anandiyankha nati, Lembera masomphenyawo, nuwachenutse pamagome, kuti awawerenge mofulumira.

3Dan. 10.14; Aheb. 10.37Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.

4Yoh. 3.36; Aro. 1.17; Agal. 3.11; Aheb. 10.38Taonani, moyo wake udzikuza, wosaongoka m'kati mwake; koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.

5Ndiponso vinyo ngwonyenga, ngati munthu wodzikuza, wosakhala kwao; wakukulitsa chikhumbo chake ngati kunsi kwa manda, akunga imfa, yosakhuta, koma adzisonkhanitsira amitundu onse, nadzimemezera mitundu yonse ya anthu.

6Mik. 2.4Kodi sadzamnenera fanizo onsewo, ndi mwambi womnyodola, ndi kuti, Tsoka iye wochulukitsa zimene sizili zake? Mpaka liti? Iye wodzisenzera zigwiriro.

7Sadzauka kodi modzidzimuka iwo amene adzakuluma, ndi kugalamuka iwo amene adzakugwedezetsa; ndipo udzakhala zofunkha zao?

8Yes. 33.1Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitikira dziko, mudzi, ndi onse okhalamo.

9Tsoka iye wakupindulitsira nyumba yake phindu loipa, kuti aike chisanja chake ponyamuka, kuti alanditsidwe m'dzanja la choipa!

10Wapangira nyumba yako chamanyazi, pakuononga mitundu yambiri ya anthu, ndipo wachimwira moyo wako.

11Pakuti mwala wa m'khoma ufuula, ndi mtanda wa kuphaso udzauvomereza.

12 Yer. 22.13 Tsoka iye wakumanga mudzi ndi mwazi, nakhazikitsa mudzi ndi chisalungamo!

13Taonani, sichichokera kwa Yehova wa makamu kodi kuti mitundu ya anthu ingogwirira moto ntchito, ndi anthu angodzilemetsa pa zopanda pake?

14Yes. 11.9Pakuti dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi amphimba pansi pa nyanja.

15 Hos. 7.5 Tsoka wakuninkha mnzake chakumwa, ndi kuonjezako mankhwala ako, ndi kumledzeretsa, kuti upenyerere manyazi ao!

16Udzazidwa nao manyazi m'malo mwa ulemerero; imwa iwenso, nukhale wosadulidwa; chikho cha dzanja lamanja la Yehova chidzatembenukira iwe, ndi kusanza kwa manyazi kudzakhala pa ulemerero wako.

17Pakuti chiwawa chidachitikira Lebanoni chidzakukuta, ndi chionongeko cha nyama chidzakuopsa; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitidwira dziko, mudzi, ndi onse okhalamo.

18 Yes. 44.9-10 Apindulanji nalo fano losema, kuti wakulipanga analisema; fano loyenga ndi mphunzitsi wamabodza, kuti wakulipanga alikhulupirira, atapanga mafano osanena mau?

19Mas. 135.15-17Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka! Kodi ichi chiphunzitsa? Taona chakutidwa ndi golide ndi siliva, ndi m'kati mwake mulibe mpweya konse.

20Mas. 11.4; Zef. 1.7; Zek. 2.13Koma Yehova ali m'Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help