1 Mac. 15.2 Pamenepo popita zaka khumi ndi zinai ndinakweranso kunka ku Yerusalemu pamodzi ndi Barnabasi, ndinamtenganso Tito andiperekeze.
2Mac. 15.12; Afi. 2.16Koma ndinakwera kunkako movumbulutsa; ndipo ndinawauza Uthenga Wabwino umene ndiulalikira kwa amitundu; koma m'tseri kwa iwo omveka, kuti kapena ndingathamange, kapena ndikadathamanga chabe.
3Komatu ngakhale Tito, amene anali ndi ine, ndiye Mgriki, sanamkakamiza adulidwe;
4Mac. 15.1, 24; Agal. 3.25; 5.1, 13ndicho chifukwa cha abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tili nao mwa Khristu Yesu, kuti akatichititse ukapolo.
5Agal. 3.1Koma sitidawafumukira mowagonjera ngakhale ora limodzi; kuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi inu.
6Mac. 10.34Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati anali otani kale, kulibe kanthu kwa ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu) iwo omvekawo sanandionjezera ine kanthu;
7Mac. 13.46; Aro. 11.13koma pena, pakuona kuti anaikiza kwa ine Uthenga Wabwino wa kusadulidwa, monga kwa Petro Uthenga Wabwino wa mdulidwe
8Akol. 1.29(pakuti Iye wakuchita mwa Petro kumtuma kwa odulidwa anachitanso mwa ine kundituma kwa amitundu);
9Aro. 15.15ndipo pakuzindikira chisomocho chinapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Barnabasi dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;
10Mac. 24.17pokhapo kuti tikumbukire aumphawi; ndicho chomwe ndinafulumira kuchichita.
11 Mac. 15.1 Koma pamene Kefa anadza ku Antiokeya ndinatsutsana naye pamaso pake, pakuti anatsutsika wolakwa.
12Mac. 10.28Pakuti asanafike ena ochokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi amitundu; koma atadza iwo, anadzibweza, ndi kudzipatula yekha, pakuopa iwo a ku mdulidwe.
13Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Barnabasinso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao.
14Mac. 10.28Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukakamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?
15Ife ndife Ayuda pachibadwidwe, ndipo sitili ochimwa a kwa amitundu;
16Mac. 13.38-39koma podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama pa ntchito ya lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu, ifedi tinakhulupirira kwa Khristu Yesu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro cha Khristu, ndipo si ndi ntchito za lamulo; pakuti palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo.
171Yoh. 3.8-9Koma ngati ife, pofuna kuyesedwa olungama mwa Khristu, tipezedwanso tili ochimwa tokha, kodi Khristu ali mtumiki wa uchimo chifukwa chake? Msatero ai.
18Pakuti ngati izi zomwezi ndazigumula ndidzimanganso, ndidzitsimikizira ndekha ndili wolakwa.
19Aro. 7.4, 6Pakuti ine mwa lamulo ndafa kulamulo, kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu.
20Aro. 6.6; 2Ako. 5.15; Aef. 5.2 Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
21Aheb. 7.11Sindichiyesa chopanda pake chisomo cha Mulungu; pakuti ngati chilungamo chili mwa lamulo, Khristu adafa chabe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.