MASALIMO 37 - Buku Lopatulika Bible 2014

Kusangalala kwa ochimwa kudzatha, olungama akhalitsa nathandizidwa ndi MulunguSalimo la Davide.

1 Miy. 24.1, 19 Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa,

usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama.

2 Mas. 90.5-6 Pakuti adzawamweta msanga monga udzu,

ndipo adzafota monga msipu wauwisi.

3Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma;

khala m'dziko, ndipo tsata choonadi.

4 Yes. 58.1 Udzikondweretsenso mwa Yehova;

ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.

5 Mat. 6.25 Pereka njira yako kwa Yehova;

khulupiriranso Iye, adzachichita.

6 Yes. 58.8, 10 Ndipo adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika,

ndi kuweruza kwako monga usana.

7 Mas. 37.1, 8; 62.1 Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye;

usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake,

chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.

8Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo;

usavutike mtima ungachite choipa.

9 Mas. 37.11, 22, 29 Pakuti ochita zoipa adzadulidwa;

koma iwo akuyembekeza Yehova,

iwowa adzalandira dziko lapansi.

10Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti;

inde, udzayang'anira mbuto yake, nudzapeza palibe.

11 Mat. 5.5 Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi;

nadzakondwera nao mtendere wochuluka.

12Woipa apangira chiwembu wolungama,

namkukutira mano.

13 1Sam. 26.10 Ambuye adzamseka,

popeza apenya kuti tsiku lake likudza.

14Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao;

alikhe ozunzika ndi aumphawi,

aphe amene ali oongoka m'njira.

15Lupanga lao lidzalowa m'mtima mwao momwe,

ndipo mauta ao adzathyoledwa.

16 Miy. 15.16; 1Tim. 6.6 Zochepa zake za wolungama zikoma

koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri.

17Pakuti manja a oipa adzathyoledwa,

koma Yehova achirikiza olungama.

18Yehova adziwa masiku a anthu angwiro;

ndipo chosiyira chao chidzakhala chosatha.

19Sadzachita manyazi m'nyengo yoipa,

ndipo m'masiku a njala adzakhuta.

20Pakuti oipa adzatayika,

ndipo adani ake a Yehova adzanga mafuta a anaankhosa;

adzanyeka, monga utsi adzakanganuka.

21Woipa akongola, wosabweza,

koma wolungama achitira chifundo, napereka.

22Pakuti iwo amene awadalitsa adzalandira dziko lapansi;

koma iwo amene awatemberera adzadulidwa.

23 1Sam. 2.9 Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu;

ndipo akondwera nayo njira yake.

24 Mik. 7.8; 2Ako. 4.9 Angakhale akagwa, satayikiratu,

pakuti Yehova agwira dzanja lake.

25Ndinali mwana ndipo ndakalamba;

ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa,

kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.

26Tsiku lonse achitira chifundo, nakongoletsa;

ndipo mbumba zake zidalitsidwa.

27 Yes. 1.16-17 Siyana nacho choipa, nuchite chokoma,

nukhale nthawi zonse.

28 Mas. 97.10; Yes. 14.20 Pakuti Yehova akonda chiweruzo,

ndipo sataya okondedwa ake.

Asungika kosatha,

koma adzadula mbumba za oipa.

29Olungama adzalandira dziko lapansi,

nadzakhala momwemo kosatha.

30 Mat. 12.35 Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru,

ndi lilime lake linena chiweruzo.

31 Yes. 51.7 Malamulo a Mulungu wake ali mumtima mwake;

pakuyenda pake sadzaterereka.

32Woipa aunguza wolungama,

nafuna kumupha.

33Yehova sadzamsiya m'dzanja lake;

ndipo sadzamtsutsa poweruzidwa iye.

34 Mas. 27.14; Miy. 20.22 Yembekeza Yehova, nusunge njira yake,

ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko.

Pakudulidwa oipa udzapenya.

35Ndapenya woipa, alikuopsa,

natasa monga mtengo wauwisi wanzika.

36Koma anapita ndipo taona, kwati zii;

ndipo ndinampwaira osampeza.

37 Yes. 32.17 Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima!

Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere.

38Koma olakwa adzaonongeka pamodzi;

matsiriziro a oipa adzadulidwa.

39 Mas. 9.9 Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova,

Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso.

40 Yes. 31.5 Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa;

awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa,

chifukwa kuti anamkhulupirira Iye.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help