1Lemekeza Yehova, moyo wanga;
ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.
2Lemekeza Yehova, moyo wanga,
ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi:
3 Mrk. 2.5, 10-11; Luk. 7.47 Amene akhululukira mphulupulu zako zonse;
nachiritsa nthenda zako zonse;
4 Mas. 56.13 amene aombola moyo wako ungaonongeke;
nakuveka korona wa chifundo ndi nsoni zokoma:
5 Yes. 40.31 Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino;
nabweza ubwana wako unge mphungu.
6 Mas. 146.7 Yehova achitira onse osautsidwa
chilungamo ndi chiweruzo.
7 Mas. 147.19 Analangiza Mose njira zake,
ndi ana a Israele machitidwe ake.
8 Num. 14.18; Neh. 9.17 Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo,
wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chochuluka.
9 Yes. 57.16 Sadzatsutsana nao nthawi zonse;
ndipo sadzasunga mkwiyo wake kosatha.
10 Ezr. 9.13 Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu,
kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.
11 Aef. 3.18-19 Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi,
motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.
12 Yes. 43.25 Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo,
momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.
13 Mala. 3.17 Monga atate achitira ana ake chifundo,
Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.
14 Mas. 78.39 Popeza adziwa mapangidwe athu;
akumbukira kuti ife ndife fumbi.
15 Mas. 90.5-6 Koma munthu, masiku ake akunga udzu;
aphuka monga duwa la kuthengo.
16Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe:
Ndi malo ake salidziwanso.
17 Eks. 20.6 Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba
kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye,
ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;
18kwa iwo akusunga chipangano chake,
ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita.
19Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba;
ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo.
20 Mat. 6.10 Lemekezani Yehova, inu angelo ake;
a mphamvu zolimba, akuchita mau ake,
akumvera liu la mau ake.
21 Aheb. 1.14 Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse;
inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye.
22Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse,
ponseponse pali ufumu wake:
Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.