ESTERE 9 - Buku Lopatulika Bible 2014

Ayuda awapha adani ao

1Mwezi wakhumi ndi chiwiri tsono, ndiwo mwezi wa Adara, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, mau a mfumu ndi lamulo lake ali pafupi kuchitika, tsikuli adani a Ayuda anayesa kuwachitira ufumu, koma chinasinthika; popeza Ayuda anachitira ufumu iwo odana nao;

2Est. 8.11, 17pakuti Ayuda anasonkhana pamodzi m'midzi mwao, m'maiko onse a mfumu Ahasuwero, kuwathira manja ofuna kuwachitira choipa, ndipo palibe munthu analimbika pamaso pao; popeza kuopsa kwao kudawagwera mitundu yonse ya anthu.

3Ndipo akalonga onse a maikowo, ndi akazembe, ndi ziwanga, ndi iwo ochita ntchito ya mfumu, anathandiza Ayuda; popeza kuopsa kwa Mordekai kudawagwera.

42Sam. 3.1Pakuti Mordekai anali wamkulu m'nyumba ya mfumu, ndi mbiri yake idabuka m'maiko onse; pakuti munthuyu Mordekai anakulakulabe.

5Ndipo Ayuda anakantha adani ao onse, kuwakantha ndi lupanga, ndi kuwapulula, nachitira odana nao monga anafuna.

6Ndipo m'chinyumba cha ku Susa Ayuda anakantha, naononga amuna mazana asanu.

7Napha Parasadata, ndi Dalifoni, ndi Asipata,

8ndi Porata, ndi Adaliya, ndi Aridata,

9ndi Parimasta, ndi Arisai, ndi Aridai, ndi Vaizata,

10Est. 5.11; 8.11ana amuna khumi a Hamani mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande zofunkha.

11Tsiku lomwelo anabwera nacho kwa mfumu chiwerengo cha iwo ophedwa m'chinyumba cha ku Susa.

12Est. 7.2Ndipo mfumu inati kwa mkazi wamkulu Estere, Ayuda adapha, naononga amuna mazana asanu m'chinyumba cha ku Susa, ndi ana amuna khumi a Hamani; nanga m'maiko ena a mfumu munachitikanji? Pempho lanu ndi chiyani tsono? Lidzachitikira inu; kapena mufunanjinso? Kudzachitika.

132Sam. 21.6, 9Nati Estere, Chikakomera mfumu, alole Ayuda okhala m'Susa achite ndi mawa lomwe monga mwa lamulo la lero; ndi ana amuna khumi a Hamani apachikidwe pamtengo.

14Ndipo mfumu inati azichita motero, nalamulira m'Susa, napachikidwa ana amuna khumi a Hamani.

15Ndipo Ayuda okhala m'Susa anasonkhana pamodzi, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wa Adara, napha amuna mazana atatu m'Susa; koma sanalande zofunkha.

16Est. 8.11Nasonkhana pamodzi Ayuda ena okhala m'maiko a mfumu, nalimbikira moyo wao, napumula pa adani ao, nawapha a iwo odana nao zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu; koma sanalande zofunkha.

17Chinachitika ichi tsiku lakhumi ndi chitatu la mwezi wa Adara, ndi tsiku lake lakhumi ndi chinai anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera.

18Koma Ayuda okhala m'Susa anasonkhana tsiku lakhumi ndi chitatu ndi lakhumi ndi chinai, ndi pa tsiku lakhumi ndi chisanu anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera.

19Neh. 8.10, 12Chifukwa chake Ayuda a kumilaga, okhala m'midzi yopanda malinga, amaliyesa tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wa Adara tsiku la kukondwera ndi madyerero, ndi tsiku lokoma, ndi lakutumizirana magawo.

Masungidwe a tsiku la Purimu

20Ndipo Mordekai analembera izi, natumiza akalata kwa Ayuda onse okhala m'maiko onse a mfumu Ahasuwero, a kufupi ndi a kutali,

21kuwalimbikitsira, asunge tsiku lakhumi ndi chinai, mwezi wa Adara, ndi tsiku lake lakhumi ndi chisanu lomwe, chaka ndi chaka,

22Est. 9.19; Mas. 30.11ndiwo masiku amene Ayuda anapumula pa adani ao; ndi mwezi wachisoni unawasandulikira wakukondwera, ndi wamaliro ukhale tsiku lokoma, awayese masiku amadyerero ndi akukondwera, akutumizirana magawo, ndi akupatsa zaufulu kwa osauka.

23Ndipo Ayuda anavomereza kuchita monga umo adayambira, ndi umo Mordekai adawalembera;

24Est. 3.6-7popeza Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda onse, adapangira Ayuda chiwembu kuwaononga, naombeza Puri, ndiwo ula, kuwatha ndi kuwaononga;

25Est. 7.10; Mas. 7.16koma pofika mlanduwo kwa mfumu, anati mwa akalata kuti chiwembu chake choipa adachipangira Ayuda, chimbwerere mwini; ndi kuti iye ndi ana amuna ake apachikidwe pamtengo.

26Est. 9.20Chifukwa chake anatcha masikuwa Purimu, ndilo dzina la ulawo. Momwemo, chifukwa cha mau onse a kalatayo, ndi izi adaziona za mlanduwo, ndi ichi chidawadzera,

27Ayuda anakhazikitsa ichi, nadzilonjezetsa okha, ndi mbeu yao, ndi onse akuphatikana nao, chingalekeke, kuti adzasunga masiku awa awiri monga mwalembedwa, ndi monga mwa nyengo yao yoikika, chaka ndi chaka;

28ndi kuti masikuwa adzakumbukika ndi kusungika mwa mibadwo yonse, banja lililonse, dziko lililonse, ndi mudzi uliwonse; ndi kuti masiku awa sadzalekeka mwa Ayuda, kapena kusiyidwa chikumbukiro chao mwa mbeu yao.

29Pamenepo Estere mkazi wamkulu mwana wa Abihaili, ndi Mordekai Myuda, analembera molamulira, kukhazikitsa kalata uyu wachiwiri wa Purimu.

30Natumiza iye akalata kwa Ayuda onse, kumaiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri a ufumu wa Ahasuwero, ndiwo mau a mtendere ndi choonadi;

31Est. 4.3, 16kukhazikitsa masiku awa a Purimu m'nyengo zao, m'mene Mordekai Myuda ndi mkazi wamkulu Estere adawakhazikitsira; ndi umo anadzikhazikitsira okha, ndi mbeu yao, kunena za kusala kwao, ndi kufuula kwao.

32Ndipo kunena kwake kwa Estere kunakhazikitsa mau awa a Purimu; ndipo kunalembedwa m'buku.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help