MASALIMO 9 - Buku Lopatulika Bible 2014

Ayamikira chipulumutso chachikuluKwa Mkulu wa Nyimbo; pa Muti-Labeni. Salimo la Davide.

1Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse;

ndidzawerengera zodabwitsa zanu zonse.

2

lalikirani mwa anthu ntchito zake.

12 Gen. 9.5 Pakuti Iye wofuna chamwazi awakumbukira;

saiwala kulira kwa ozunzika.

13Ndichitireni chifundo, Yehova;

penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo,

inu wondinyamula kundichotsa kuzipata za imfa.

14 Mas. 13.5 Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse;

pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni,

ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu.

15 Mas. 7.15-16 Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba,

lakodwa phazi lao muukonde anautcha.

16 Eks. 7.5 Anadziwika Yehova, anachita kuweruza,

woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake.

17Oipawo adzabwerera kumanda,

inde amitundu onse akuiwala Mulungu.

18 Mas. 9.12 Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi,

kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzaonongeka kosatha.

19Ukani, Yehova, asalimbike munthu;

amitundu aweruzidwe pankhope panu.

20Muwachititse mantha, Yehova;

adziwe amitundu kuti ali anthu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help