MARKO 11 - Buku Lopatulika Bible 2014

Yesu alowa m'Yerusalemu alikukhala pa bulu(Mat. 21.1-11; Luk. 19.29-44; Yoh. 12.12-19)

1Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri la Azitona, anatuma awiri a ophunzira ake,

2nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye.

3Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Katini, Ambuye amfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno.

4Ndipo anachoka, napeza mwana wa bulu womangidwa pakhomo, pabwalo m'khwalala, nammasula iye.

5Ndipo ena akuima kumeneko ananena nao, Muchita chiyani ndi kumasula mwana wa bulu?

6Ndipo anati kwa iwo monga momwe ananena Yesu: ndipo anawalola iwo apite naye.

7Ndipo anabwera naye mwana wa bulu kwa Yesu, naika zovala zao pa iye, ndipo Iye anakhala pamenepo.

8Ndimo ambiri anayala zovala zao panjira; ndi ena zitsamba, anazidula m'minda.

9Ubatizo wa Yohane(Mat. 21.23-27; Luk. 20.1-8)

27Ndipo iwo anadzanso ku Yerusalemu; ndipo m'mene Iye anali kuyenda m'Kachisi, anafika kwa Iye ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu;

28nanena naye, Izi muzichita ndi ulamuliro wotani? Kapena anakupatsani ndani ulamuliro uwu wakuchita izi?

29Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani mau amodzi, mundiyankhe Ine, ndipo ndidzakuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu zimenezi.

30Ubatizo wa Yohane uchokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu? Mundiyankhe.

31Ndipo anatsutsana mwa iwo okha, nanena, Tikati, Kumwamba; adzanena Iye, Ndipo simunakhulupirira iye bwanji?

32Mat. 14.5Koma tikati, Kwa anthu, anaopa anthuwo; pakuti onse anamuyesa Yohane mneneri ndithu.

33Ndipo iwo anamyankha Yesu, ananena nao, Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu zimenezi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help