MACHITIDWE A ATUMWI 20 - Buku Lopatulika Bible 2014

Paulo apitanso ku Masedoniya, ndi Grisi, ndi Asiya

1Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitana ophunzirawo, ndipo m'mene anawachenjeza, analawirana nao, natuluka kunka ku Masedoniya.

2Ndipo m'mene atapitapita m'mbali zijazo, nawachenjeza, anadza ku Grisi.

3Mau a Paulo kwa akulu a ku Efeso

17Ndipo pokhala ku Mileto anatuma ku Efeso, naitana akulu a Mpingo.

18Ndipo pamene anafika kuli iye, anati kwa iwo, Mudziwa inu kuyambira tsiku loyamba ndinafika ku Asiya, makhalidwe anga pamodzi ndi inu nthawi yonse,

19Mac. 20.3wotumikira Ambuye ndi kudzichepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda;

20Mac. 20.27kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba zanu,

21Mrk. 1.15ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

22Ndipo, taonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zimene zidzandigwera ine kumeneko;

23Mac. 9.16; 21.4, 11koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m'midzi yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.

24Mac. 21.13; Agal. 1.1Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.

25Mac. 20.38Ndipo tsopano, taonani, ndidziwa ine kuti inu nonse amene ndinapitapita mwa inu kulalikira ufumuwo, simudzaonanso nkhope yanga.

26Mac. 18.6Chifukwa chake ndikuchitirani umboni lero lomwe, kuti ndilibe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.

27Mac. 20.20Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.

28Aef. 1.7, 14; 1Pet. 5.2Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.

29Mat. 7.15Ndidziwa ine kuti, nditachoka ine, adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo;

30ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.

31Mac. 19.10Chifukwa chake dikirani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindinaleka usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi.

32Aef. 1.14, 18Ndipo tsopano ndikuikizani kwa Mulungu, ndi kwa mau a chisomo chake, chimene chili ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu cholowa mwa onse oyeretsedwa.

331Sam. 12.3; 1Ako. 9.12Sindinasirira siliva, kapena golide, kapena chovala cha munthu aliyense.

34Mac. 18.3Mudziwa inu nokha kuti manja anga awa anatumikira zosowa zanga, ndi za iwo akukhala ndi ine.

351Sam. 12.3; 1Ako. 9.12M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.

36 Mac. 21.5 Ndipo m'mene ananena izi, anagwada pansi, napemphera ndi iwo onse.

37Ndipo onsewa analira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pake, nampsompsona,

38Mat. 6.10nalira makamaka chifukwa cha mau adanenawa, kuti sadzaonanso nkhope yake. Ndipo anamperekeza iye kungalawa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help