MASALIMO 27 - Buku Lopatulika Bible 2014

Davide atamadi Yehova, naliradi kuyanjana ndi MulunguSalimo la Davide.

1 Eks. 15.2; Mas. 62.2; Yes. 12.3; 60.19-20 Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa;

ndidzaopa yani?

Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga;

ndidzachita mantha ndi yani?

2Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga,

inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.

3 Mas. 3.6 Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole,

mtima wanga sungachite mantha;

ingakhale nkhondo ikandiukira,

inde pomweponso ndidzakhulupirira.

4 Mas. 26.8 Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova,

ndidzachilondola ichi,

Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,

kupenya kukongola kwake kwa Yehova

ndi kufunsitsa m'Kachisi wake.

5 Yes. 4.6 Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake,

adzandibisa m'tsenjezi mwa chihema chake;

pathanthwe adzandikweza.

6 Mas. 3.3; Aef. 5.19 Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka

pamwamba pa adani anga akundizinga;

ndipo ndidzapereka m'chihema mwake

nsembe za kufuula mokondwera;

ndidzaimba, inde, ndidzaimbira Yehova zomlemekeza.

7Imvani, Yehova, liu langa pofuula ine;

mundichitirenso chifundo ndipo mundivomereze.

8 Mas. 105.4 Pamene munati, Funani nkhope yanga;

mtima wanga unati kwa Inu.

Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna.

9 Mas. 69.17 Musandibisire ine nkhope yanu;

musachotse kapolo wanu ndi kukwiya.

Inu munakhala thandizo langa;

musanditaye, ndipo musandisiye

Mulungu wa chipulumutso changa.

10 Yes. 49.15 Pakuti wandisiya atate wanga ndi amai wanga,

koma Yehova anditola.

11 Mas. 25.4 Mundiphunzitse njira yanu, Yehova,

munditsogolere pa njira yachidikha,

chifukwa cha adani anga.

12 Mas. 35.25; Mat. 26.59-60 Musandipereke ku chifuniro cha akundisautsa,

chifukwa zinandiukira mboni zonama

ndi iwo akupumira zachiwawa.

13Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova

m'dziko la amoyo, ndikadatani!

14 Yos. 1.6, 9, 18; Yes. 25.9 Yembekeza Yehova,

limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako;

inde, yembekeza Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help