NUMERI 33 - Buku Lopatulika Bible 2014

Za ulendo wa Aisraele pakati pa Ramsesi ndi Sitimu

1Maulendo a ana a Israele amene anatuluka m'dziko la Ejipito monga mwa makamu ao, ndi dzanja la Mose ndi Aroni, ndi awa.

2Ndipo Mose analembera matulukidwe ao monga mwa maulendo ao, monga mwa mau a Yehova; ndipo maulendo ao ndi awa monga mwa matulukidwe ao.

3Eks. 12Ndipo anachokera ku Ramsesi mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi woyamba; atachita Paska m'mawa mwake ana a Israele, anatuluka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aejipito onse,

4Yes. 19.1pamene Aejipito analikuika oyamba kubadwa ao onse, amene Yehova adawakantha; Yehova adaweruzanso milungu yao.

5Ndipo ana a Israele anachokera ku Ramsesi, nayenda namanga ku Sukoti.

6Nachokera ku Sukoti, nayenda namanga m'Etamu, ndiko ku malekezero a chipululu.

7Ndipo anachokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwake kwa Baala-Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli.

8Eks. 14.22Ndipo anachokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'chipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, namanga m'Mara.

9Ndipo anachokera ku Mara, nayenda nafika ku Elimu, ku Elimu ndiko kuli akasupe khumi ndi awiri a madzi, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; namanga iwo komweko.

10Ndipo anachokera ku Elimu, nayenda namanga ku Nyanja Yofiira.

11Eks. 16Nachokera ku Nyanja Yofiira, nayenda namanga m'chipululu cha Sini.

12Nachokera ku chipululu cha Sini, nayenda namanga m'Dofika.

13Nachokera ku Dofika, nayenda namanga m'Alusi.

14Eks. 17Nachokera ku Alusi, nayenda namanga m'Refidimu; kumeneko kunalibe madzi kuti anthu amwe.

15Eks. 19Ndipo anachokera ku Refidimu, nayenda namanga m'chipululu cha Sinai.

16Nachokera ku chipululu cha Sinai, nayenda namanga m'Kibroti-Hatava.

17Nachokera ku Kibroti-Hatava, nayenda namanga m'Hazeroti.

18Nachokera ku Hazeroti, nayenda namanga m'Ritima.

19Nachokera ku Ritima, nayenda namanga m'Rimoni-Perezi.

20Nachokera ku Rimoni-Perezi, nayenda namanga m'Libina.

21Nachokera ku Libina, nayenda namanga m'Risa.

22Nachokera Risa, nayenda namanga m'Kehelata.

23Nachokera ku Kehelata, nayenda namanga m'phiri la Sefera.

24Nachokera kuphiri la Sefera, nayenda namanga m'Harada.

25Nachokera ku Harada, nayenda namanga m'Makeloti.

26Nachokera ku Makeloti, nayenda namanga m'Tahata.

27Nachokera ku Tahata, nayenda namanga m'Tera.

28Nachokera ku Tera, nayenda namanga m'Mitika.

29Nachokera ku Mitika, nayenda namanga m'Hasimona.

30Nachokera ku Hasimona, nayenda namanga m'Meseroti.

31Nachokera ku Meseroti, nayenda namanga m'Bene-Yaakani.

32Nachokera ku Bene-Yaakani, nayenda namanga m'Hori Hagidigadi.

33Nachokera ku Hori Hagidigadi, nayenda namanga m'Yotibata.

34Nachokera ku Yotibata, nayenda namanga m'Aborona.

351Maf. 9.26Nachokera ku Aborona, nayenda namanga m'Eziyoni-Gebere.

36Nachokera ku Eziyoni-Gebere, nayenda namanga m'chipululu cha Zini (ndiko Kadesi).

37Nachokera ku Kadesi, nayenda namanga m'phiri la Hori, ku malekezero a dziko la Edomu.

38Num. 20.25Ndipo Aroni wansembe anakwera m'phiri la Hori pa mau a Yehova, nafa komweko, atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito zaka makumi anai, mwezi wachisanu, tsiku loyamba la mwezi.

39Ndipo Aroni ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi awiri kudza zitatu pakufa iye m'phiri la Hori.

40Ndipo Mkanani, mfumu ya Aradi, wakukhala kumwera m'dziko la Kanani, anamva za kudza kwao kwa ana a Israele.

41Ndipo anachokera kuphiri la Hori, nayenda namanga m'Zalimona.

42Nachokera ku Zalimona, nayenda namanga m'Punoni.

43Nachokera ku Punoni, nayenda namanga m'Oboti.

44Nachokera ku Oboti, nayenda namanga m'Iyeabarimu, m'malire a Mowabu.

45Nachokera ku Iyimu, nayenda namanga m'Diboni Gadi.

46Nachokera ku Diboni Gadi, nayenda namanga m'Alimoni-Dibulataimu.

47Nachokera ku Alimoni-Dibulataimu, nayenda namanga m'mapiri a Abarimu, chakuno cha Nebo.

48Nachokera ku mapiri a Abarimu, nayenda namanga m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko.

49Ndipo anamanga pa Yordani, kuyambira ku Beteyesimoti kufikira ku Abele-Sitimu m'zidikha za Mowabu.

Aisraele azipirikitsa eni dziko la Kanani

50Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko, nati,

51Yos. 3.17Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutaoloka Yordani kulowa m'dziko la Kanani,

52mupirikitse onse okhala m'dziko pamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse;

53ndipo mulande dziko, ndi kukhala m'mwemo, pakuti ndinakupatsani inu dzikoli likhale lanulanu.

54Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu.

55Yos. 23.13; Ower. 2.2-3Koma mukapanda kupirikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakuvutani m'dziko limene mukhalamo.

56Ndipo kudzakhala kuti monga ndinayesa kuchitira iwowa, ndidzakuchitirani inu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help