1Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
2Ana a Israele achite Paska pa nyengo yoikidwa.
3Tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, muziuchita, pa nyengo yake yoikidwa; muuchite monga mwa malemba ake onse, ndi maweruzo ake onse.
4Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, kuti achite Paska.
5Yos. 5.10Ndipo anachita Paska mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo m'chipululu cha Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israele anachita.
6Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoze kuchita Paska tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;
7nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, pakati pa ana a Israele?
8Num. 27.5Ndipo Mose ananena nao, Baimani; ndimve chouza Yehova za inu.
9Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
10Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Angakhale munthu wa inu kapena wa mibadwo yanu, adetsedwa, chifukwa cha mtembo, kapena pokhala paulendo, koma azichitira Yehova Paska.
11Mwezi wachiwiri, tsiku lake lakhumi ndi chinai, madzulo, auchite; audye ndi mkate wopanda chotupitsa ndi msuzi wowawa.
12Eks. 12.46; Yoh. 19.36Asasiyeko kufikira m'mawa, kapena kuthyolapo fupa; auchite monga mwa lemba lonse la Paska.
13Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.
14Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakachitira Yehova Paska, azichita monga mwa lemba la Paska, ndi monga mwa chiweruzo chake; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko.
Mtambo pamwamba pa Kachisi15Ndipo tsiku loutsa Kachisi mtambo unaphimba Kachisi, ndiwo chihema chokomanako; ndicho chihema chaumboni, ndipo madzulo padaoneka pa Kachisi ngati moto, kufikira m'mawa.
16Kudatero kosalekeza; mtambo umachiphimba, ndi moto umaoneka usiku.
17Ndipo pokwera mtambo kuchokera kuchihema, utatero ana a Israele amayenda ulendo wao; ndipo pamalo pokhala mtambo, pamenepo ana a Israele amamanga mahema ao.
181Ako. 10.1Pakuwauza Yehova ana a Israele amayenda ulendo, powauza Yehova amamanga mahema ao; masiku onse mtambo ukakhala pamwamba pa Kachisi amakhala m'chigono.
19Ndipo pakukhalitsa mtambo masiku ambiri pamwamba pa Kachisi, pamenepo ana a Israele anasunga udikiro wa Yehova osayenda ulendo.
20Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa Kachisi masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'chigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova.
21Koma mtambo ukakhala kuyambira madzulo kufikira m'mawa; pokwera mtambo m'mawa, ayenda ulendo.
22Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa Kachisi ndi kukhalapo, ana a Israele anakhala m'chigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo.
23Mat. 6.10Powauza Yehova amanga mahema, powauza Yehova ayenda ulendo; anasunga udikiro wa Yehova powauza Yehova mwa dzanja la Mose.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.